Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 30:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo kunali, pakufika Davide ndi anthu ake ku Zikilagi tsiku lachitatu, Aamaleke adaponya nkhondo yovumbulukira kumwera, ndi ku Zikilagi, nathyola Zikilagi nautentha ndi moto;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Patapita masiku aŵiri, Davide ndi anthu ake adafika ku Zikilagi. Tsono adapeza kuti Aamaleke anali atasakaza dera la kumwera kwa Yuda ndi kuthira nkhondo mzinda wa Zikilagi. Adagonjetsa mzindawo, nauthira moto.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Pa tsiku lachitatu, Davide ndi anthu ake anakafika ku Zikilagi. Tsono anapeza Aamaleki atawononga kale dera la Negevi ndi Zikilagi. Anathira nkhondo mzinda wa Zikilagi ndi kuwutentha ndi moto.

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 30:1
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Isaki anadzera njira ya Beere-Lahai-Roi; chifukwa kuti anakhala iye m'dziko la kumwera.


Ndipo kunali atamwalira Saulo, pamene Davide anabwera atawapha Aamaleke, ndipo Davide atakhala ku Zikilagi masiku awiri;


pa tsiku lachitatu, onani, munthu anatuluka ku zithando za Saulo, ali ndi zovala zake zong'ambika, ndi dothi pamutu pake; ndipo kunatero kuti iye, pofika kwa Davide, anagwa pansi namgwadira.


Nanena, Ndiwe yani? Ndipo ndinayankha kuti, Ndine Mwamaleke.


Ndipo anyamata ake onse anapita naye limodzi; ndi Akereti ndi Apeleti, ndi Agiti onse, anthu mazana asanu ndi limodzi omtsata kuchokera ku Gati, anapita pamaso pa mfumu.


Ndipo anathandiza Davide aponyane nalo gulu la achifwamba, pakuti onse ndiwo ngwazi zamphamvu, nakhala atsogoleri m'khamu la nkhondo.


Pakuti nthawi yomweyo anadza kwa Davide kumthandiza, mpaka kunali nkhondo yaikulu, ngati nkhondo ya Mulungu.


anatenga anthu onse, nanka kukamenyena ndi Ismaele mwana wa Netaniya, nampeza pamadzi ambiri a mu Gibiyoni.


Koma Yehova anati kwa Yoswa, Usaope chifukwa cha iwowa; pakuti mawa, dzuwa lino ndidzawapereka onse ophedwa pamaso pa Israele; udzawadula mitsindo akavalo ao, ndi kutentha agaleta ao ndi moto.


ndi Zikilagi, ndi Madimana ndi Sanisana;


Ndipo Saulo anakantha Aamaleke, kuyambira pa Havila, dera la ku Suri, chili pandunji pa Ejipito.


Namtenga wamoyo Agagi, mfumu ya Aamaleke, naononga konsekonse anthu onse ndi lupanga lakuthwa.


Ndipo Akisi anampatsa Zikilagi tsiku lomweli; chifukwa chake Zikilagi ndi wa mafumu a Yuda kufikira lero lomwe.


Chifukwa chake ulawirire m'mawa pamodzi ndi anyamata a mbuye wako amene anabwera nawe; ndipo mutauka m'mawa, mumuke kutacha.


Chomwecho Davide analawirira, iye ndi anthu ake, kuti amuke m'mawa ndi kubwera ku dziko la Afilisti. Ndipo Afilisti anakwera Yezireele.


Koma akalonga a Afilisti anapsa naye mtima; nanena naye akalonga a Afilisti, Bwezani munthuyu, abwerere kumalo kwake kumene munamuikako, asatsikire nafe kunkhondo, kuti kunkhondoko angasanduke mdani wathu; pakuti uyu adzadziyanjanitsa ninji ndi mfumu yake? Si ndi mitu ya anthu awa?


Tinathira nkhondo kumwera kwa Akereti ndi ku dziko lija la Ayuda, ndi kumwera kwa Kalebe; ndipo tinatentha mudzi wa Zikilagi ndi moto.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa