Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:45 - Buku Lopatulika

45 Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

45 Pamenepo anatsika Aamaleke, ndi Akanani, akukhala m'phirimo nawakantha, nawapha kufikira ku Horoma.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

45 Tsono Aamaleke ndi Akanani, amene ankakhala m'dziko lamapirilo, adatsika ndipo adaŵagonjetsa, ndi kuŵapirikitsa mpaka ku Horoma.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

45 Koma Aamaleki ndi Akanaani amene ankakhala ku dziko lamapirilo anatsika ndi kumenyana nawo ndipo anawakantha mʼnjira yonse mpaka ku Horima.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:45
14 Mawu Ofanana  

Munapinditsa kukamwa kwake kwa lupanga lake, osamuimika kunkhondo.


nati, Yehova walumbira: padzakhala nkhondo ya Yehova pa Amaleke m'mibadwomibadwo.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.


Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.


Ndipo Yehova ananena ndi Mose nati,


Ndipo Yehova anamvera mau a Israele, napereka Akanani; ndipo anawaononga konse ndi mizinda yao yomwe; natcha dzina lake la malowo Horoma.


Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anatuluka kukomana ndi inu, nakupirikitsani, monga zimachita njuchi, nakukanthani mu Seiri, kufikira ku Horoma.


Mmodzi akadapirikitsa zikwi, awiri akadathawitsa zikwi khumi, akadapanda kuwagulitsa Thanthwe lao, akadapanda kuwapereka Yehova.


Ndipo amuna a ku Ai anawakantha amuna, ngati makumi atatu mphambu asanu ndi mmodzi; nawapirikitsa kuyambira pachipata mpaka ku Sebarimu, nawakantha potsika; ndi mitima ya anthu inasungunuka inga madzi.


Ndipo Yuda anamuka ndi Simeoni mkulu wake, nakantha Akanani akukhala mu Zefati, nauononga konse. Koma dzina la mzindawo analitcha Horoma.


Ndipo Davide ndi anthu ake anakwera, nathira nkhondo yovumbulukira pa Agesuri, ndi Agerizi, ndi Aamaleke; pakuti awa ndiwo anthu akale m'dziko lija, njira ya ku Suri kufikira ku dziko la Ejipito.


ndi kwa iwo a ku Horoma, ndi kwa iwo a ku Borasani, ndi kwa iwo a ku Ataki;


Ndipo Afilistiwo anandandalitsa nkhondo yao pa Aisraele; ndipo pokomana nkhondo Aisraele anakanthidwa ndi Afilisti. Ndipo anapha kuthengoko anthu zikwi zinai a khamu lao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa