Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:44 - Buku Lopatulika

44 Koma anakwera pamwamba paphiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

44 Koma anakwera pamwamba pa phiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

44 Koma iwo adapitabe osasamala, nakwera ku dziko lamapiri, ngakhale kuti sadatsakane ndi Bokosi lachipangano cha Chauta, kapena ndi Mose, pochoka pamahemapo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

44 Komabe mwa maganizo awo anapita molunjika dziko la mapiri ngakhale kuti Mose sanachoke ndi Bokosi la Chipangano la Yehova pa msasa.

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:44
6 Mawu Ofanana  

Ndipo anayenda kuchokera kuphiri la Yehova ulendo wa masiku atatu; ndipo likasa la chipangano cha Yehova, linawatsogolera ulendo wa masiku atatu kuwafunira popumulira.


Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.


Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.


Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.


Pamene ndinanena ndi inu simunamvere; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kuchita modzikuza, nimunakwera kunka kumapiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa