Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Numeri 14:43 - Buku Lopatulika

43 Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

43 Pakuti Aamaleke ndi Akanani ali komweko patsogolo panu, ndipo mudzagwa ndi lupanga; popeza mwabwerera m'mbuyo osatsata Yehova, chifukwa chake Yehova sadzakhala nanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

43 Kumeneko Aamaleke ndi Akanani ali m'tsogolo mwanu, ndipo mudzaphedwa pa khondo. Chauta sadzakhala nanu, chifukwa choti mwaleka kumtsata.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

43 chifukwa kumeneko mukakumana ndi Aamaleki ndi Akanaani. Popeza mwaleka kutsata Yehova, Iyeyo sadzakhala nanu ndipo mudzaphedwa ndi lupanga.”

Onani mutuwo Koperani




Numeri 14:43
14 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe Solomoni mwana wanga, umdziwe Mulungu wa atate wako, umtumikire ndi mtima wangwiro ndi moyo waufulu; pakuti Yehova asanthula mitima yonse, nazindikira zolingirira zonse za maganizo; ukamfunafuna Iye udzampeza, koma ukamsiya Iye adzakusiya kosatha.


ndipo anatuluka kukomana naye Asa, nanena naye, Mundimvere, Asa, ndi onse Ayuda ndi Abenjamini, Yehova ali nanu; mukakhala ndi Iye, mukamfuna Iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.


Mutibwereretsa kuthawa otisautsa, ndipo akudana nafe adzifunkhira okha.


Koma iwo anapandukira ndi kumvetsa chisoni mzimu wake woyera, chifukwa chake Iye anasandulika mdani wao, nawathira nkhondo Iye yekha.


Angakhale alera ana ao, koma ndidzawasowetsa, wosatsala munthu; ndithunso tsoka iwowa, pamene ndiwachokera.


Ndipo nkhope yanga idzatsutsana nanu; kuti adani anu adzakukanthani, ndipo akudana ndi inu adzachita ufumu pa inu ndipo mudzathawa wopanda wakukulondolani.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.


Koma Aamaleke ndi Akanani akhala m'chigwamo; tembenukani mawa, nimunke ulendo wanu kuchipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.


Musakwereko, pakuti Yehova sali pakati pa inu; kuti angakukantheni adani anu.


Koma anakwera pamwamba paphiri modzikuza; koma likasa la chipangano la Yehova, ndi Mose, sanachoke kuchigono.


Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawatulukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.


M'mene anafika kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, ananena nao ndi kuti,


Mwa ichi ana a Israele sangathe kuima pamaso pa adani ao, awafulatira adani ao, pakuti aperekedwa aonongeke. Sindidzakhalanso nanu mukapanda kuononga choperekedwacho, kuchichotsa pakati pa inu.


Ndipo anati, Afilisti akugwera, Samisoni. Nagalamuka iye m'tulo take, nati, Ndizituluka ngati nthawi zina, ndi kudzitakasika. Koma sanadziwe kuti Yehova adamchokera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa