Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 10:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo amuna a ku Gibiyoni anatumira Yoswa mau kuchigono ku Giligala, ndi kuti, Musalekerere akapolo anu; mutikwerere msanga, ndi kutipulumutsa, ndi kutithandiza; pakuti mafumu onse a Aamori, akukhala kumapiri atisonkhanira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Anthu a ku Gibiyoni adatumiza mau kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja kuti, “Mbuyathu, musatitaye ife atumiki anu. Bwerani msanga mudzatithandize! Tipulumutseni! Mafumu onse a Aamori atsika mapiri kudzamenyana nafe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Koma anthu a ku Gibiyoni anatumiza uthenga kwa Yoswa ku misasa ya ku Giligala nati, “Musawataye anthu anu! Bwerani msanga mudzatipulumutse! Dzatithandizeni chifukwa mafumu a Aamori ochokera ku dziko la ku mapiri agwirizana kuti adzatithire nkhondo.”

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 10:6
14 Mawu Ofanana  

Pamenepo anamangirira bulu mbereko, nati kwa mnyamata wake, Kusa, tiye; usandilezetsa kuyendaku, ndikapanda kukuuza.


Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Pakuti Yehova ndiye woweruza wathu, Yehova ndiye wotipatsa malamulo, Yehova ndiye mfumu yathu; Iye adzatipulumutsa.


Aamaleke akhala m'dziko la kumwera; ndi Ahiti, ndi Ayebusi, ndi Aamori, akhala ku mapiri, ndi Akanani akhala kunyanja, ndi m'mphepete mwa Yordani.


Ndipo Maria ananyamuka masiku amenewa, namuka ndi changu kudziko la mapiri kumzinda wa Yuda;


Potero ndinatenga akulu a mafuko anu, amuna anzeru, ndi odziwika, ndi kuwaika akhale akulu anu, atsogoleri a zikwi, ndi atsogoleri a mazana, ndi atsogoleri a makumi asanu, ndi atsogoleri a makumi, ndi akapitao, a mafuko anu.


Pamenepo mafumu asanu a Aamori, ndiwo mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi, mfumu ya ku Egiloni anasonkhana, nakwera iwo ndi makamu ao onse namanga misasa pa Gibiyoni, nauthira nkhondo.


Pamenepo Yoswa anakwera kuchokera ku Giligala, iye ndi anthu onse a nkhondo pamodzi naye, ndi ngwazi zonse.


Ndipo anawapatsa mudzi wa Araba, ndiye atate wa Anaki, womwewo ndi Hebroni, ku mapiri a Yuda, ndi mabusa ake ozungulirapo.


Ndipo ana a Israele anamanga misasa ku Giligala; nachita Paska tsiku lakhumi ndi chinai la mwezi, madzulo, m'zidikha za Yeriko.


Ndipo Yoswa anachitirana nao mtendere napangana nao, akhale amoyo; ndi akalonga a msonkhano anawalumbirira.


Ndipo zinamuka kwa Yoswa kumisasa ku Giligala, ndipo zinati kwa iye ndi kwa amuna a Israele, Tachokera dziko lakutali, chifukwa chake mupangane nafe.


Koma anati kwa Yoswa, Ndife akapolo anu. Pamenepo Yoswa anati kwa iwo, Ndinu ayani? Ndipo mufuma kuti?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa