Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.
Masalimo 2:12 - Buku Lopatulika Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mumgonjere molapa, kuwopa kuti angakukwiyireni, ndipo inu mungaonongeke, chifukwa ukali wake umayaka msanga. Ngodala onse amene amathaŵira kwa Iye. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye; kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu, pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa. Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye. |
Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.
Ndiponso ndidasiya mu Israele anthu zikwi zisanu ndi ziwiri osagwadira Baala maondo ao, osampsompsona ndi milomo yao.
Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.
Ndidzauza za chitsimikizo: Yehova ananena ndi Ine, Iwe ndiwe Mwana wanga; Ine lero ndakubala.
Pobisalira pamaso panu mudzawabisa kwa chiwembu cha munthu, mudzawabisa iwo mumsasa kuti muwalanditse pa kutetana kwa malilime.
Wodala munthuyo wakuyesa Yehova wokhulupirika; wosasamala odzikuza, ndi opatukira kubodza.
Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
Ndipo tsopano aonjeza kuchimwa, nadzipangira mafano oyenga a siliva wao, mafano monga mwa nzeru zao, onsewo ntchito ya amisiri; anena za iwo, Anthu ophera nsembe apsompsone anaang'ombe.
lamulo lisanabale, tsiku lisanapitirire ngati mungu, usanakugwereni mkwiyo waukali wa Yehova, lisanakugwereni tsiku la mkwiyo wa Yehova.
Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.
kuti onse akalemekeze Mwana, monga alemekeza Atate. Wosalemekeza Mwana salemekeza Atate amene anamtuma Iye.
monganso kwalembedwa, kuti, Onani, ndikhazika mu Ziyoni mwala wakukhumudwa nao, ndi thanthwe lophunthwitsa; ndipo wakukhulupirira Iye sadzachita manyazi.
chifukwa cha inu amene mwa Iye mukhulupirira Mulungu wakumuukitsa Iye kwa akufa, ndi kumpatsa Iye ulemerero; kotero kuti chikhulupiriro chanu ndi chiyembekezo chanu chikhale pa Mulungu.
Chifukwa kwalembedwa m'lembo, Taona, ndiika mu Ziyoni mwala wotsiriza wa pangodya, wosankhika, wa mtengo wake; ndipo wokhulupirira Iye sadzanyazitsidwa.
Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?