Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 109:20 - Buku Lopatulika

20 Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

20 Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

20 Zimenezi zikhale chilango chochokera kwa Chauta kugwera ondineneza. Ziŵagwere amene amalankhula zoipira moyo wanga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

20 Awa akhale malipiro ochokera kwa Yehova pa onditsutsa anga, kwa iwo amene amayankhula zoyipa za ine.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 109:20
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Ahitofele, pakuona kuti sautsata uphungu wake anamanga bulu wake, nanyamuka, nanka kumzinda kwao, nakonza za pa banja lake, nadzipachika, nafa, naikidwa m'manda a atate wake.


Ndipo mfumu inanena ndi Mkusiyo, Mnyamatayo Abisalomu ali bwino? Mkusiyo nayankha, Adani a mbuye wanga mfumu, ndi onse akuukira inu kukuchitirani zoipa, akhale monga mnyamata ujayo.


Tsono mfumu inanenanso ndi Simei, Udziwa iwe choipa chonse mtima wako umadziwacho, chimene udachitira Davide atate wanga; chifukwa chake Yehova adzakubwezera choipa chako pamutu pako mwini.


Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu.


Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Pakuti adani anga alankhula za ine; ndipo iwo akulalira moyo wanga apangana upo,


Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.


Mwana wa Munthu anadza wakudya, ndi wakumwa, ndipo iwo amati, Onani munthu wakudyaidya ndi wakumwaimwa vinyo, bwenzi la amisonkho ndi ochimwa! Ndipo nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.


Koma Afarisi pakumva, anati, Uyu samatulutsa ziwanda koma ndi mphamvu yake ya Belezebulu, mkulu wa ziwanda.


Koma Yesu anati, Musamamletsa iye; pakuti palibe munthu adzachita champhamvu m'dzina langa, nadzakhoza msanga kundinenera Ine zoipa.


Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.


Chifukwa chake ndikuuzani inu, kuti palibe munthu wakulankhula mwa Mzimu wa Mulungu, anena, Yesu ngwotembereredwa; ndipo palibe wina akhoza kunena, Yesu ali Ambuye, koma mwa Mzimu Woyera.


Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa