Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 41:40 - Buku Lopatulika

40 Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

40 Uziyang'anira pa nyumba yanga, ndipo anthu anga onse adzalamulidwa mwa mau ako; pa mpando wachifumu pokha ine ndidzakuposa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

40 Iwe ndiwe amene udzalamulira dziko langa, ndipo anthu anga onse adzakumvera. Ine ndidzakupambana pa chokhachi choti ndine mfumu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

40 Iwe ukhala nduna yayikulu mu dziko langa ndipo anthu onse adzamvera zimene walamula. Ine ndekha ndiye amene ndidzakuposa mphamvu chifukwa ndimakhala pa mpando waufumu.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 41:40
16 Mawu Ofanana  

mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?


Ndipo Yuda anayandikira kwa iye nati, Mfumu, kapolo wanu aneneretu m'makutu a mbuyanga, mtima wanu usapse pokwiya ndi kapolo wanu; chifukwa muli ngati Farao.


Ndipo anamfotokozera iye kuti, Yosefe akali ndi moyo, ndipo alamulira m'dziko lonse la Ejipito. Pamenepo mtima wake unakomoka, pakuti sanawakhulupirire iwo.


Pakuti Mordekai Myuda anatsatana naye mfumu Ahasuwero, nakhala wamkulu mwa Ayuda, navomerezeka mwa unyinji wa abale ake wakufunira a mtundu wake zokoma, ndi wakunena za mtendere kwa mbeu yake yonse.


Zitatha izi, mfumu Ahasuwero anamkuza Hamani mwana wa Hamedata, wa ku Agagi, namkweza, naika mpando wake upose akalonga onse okhala naye.


ndi mtima wanga wakopeka m'tseri, ndi pakamwa panga padapsompsona dzanja langa;


Mpsompsoneni Mwanayo, kuti angakwiye, ndipo mungatayike m'njira ukayaka pang'ono pokha mkwiyo wake. Odala onse akumkhulupirira Iye.


Kodi upenya munthu wofulumiza ntchito zake? Adzaima pamaso pa mafumu, osaima pamaso pa anthu achabe.


Pamenepo Belisazara analamulira, ndipo anaveka Daniele chibakuwa, ndi unyolo wagolide m'khosi mwake, nalalikira za iye kuti ndiye wolamulira wachitatu mu ufumumo.


Pamenepo Daniele amene anaposa akuluwa ndi akalonga, popeza munali mzimu wopambana mwa iye, ndi mfumu inati imuike woyang'anira ufumu wonse.


namlanditsa iye m'zisautso zake zonse, nampatsa chisomo ndi nzeru pamaso pa Farao mfumu ya ku Ejipito; ndipo anamuika iye kazembe wa pa Ejipito ndi pa nyumba yake yonse.


Pamenepo Samuele anatenga nsupa ya mafuta, nawatsanulira pamutu pake, nampsompsona iye, nati, Sanakudzozeni ndi Yehova kodi, Mukhale mfumu ya pa cholowa chake?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa