Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao.
Genesis 20:7 - Buku Lopatulika Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.” |
Ndipo akalonga ake a Farao anamuona iye, namyamikira iye kwa Farao; ndipo anamuka ndi mkazi kunyumba kwake kwa Farao.
Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu.
koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.
Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleki, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu.
Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.
Ndipo Abimeleki analawira m'mamawa, naitana anyamata ake onse, nanena zonse zimenezo m'makutu mwao, ndipo anthu anaopa kwambiri
Mutimvere ife mfumu, ndinu kalonga wamkulu pakati pa ife; muike wakufa wanu m'manda mwathu mosankhika: palibe munthu yense wa ife adzakaniza manda ake, kuti muike wakufa wanu.
Ndipo Davide analankhula ndi Yehova pamene anaona mthenga wakudwalitsa anthu, nati, Onani ndachimwa ine, ndinachita mwamphulupulu; koma nkhosa izi zinachitanji? Dzanja lanu likhale pa ine ndi pa nyumba ya atate wanga.
Ndipo mfumu inayankha niti kwa munthu wa Mulungu, Undipembedzere Yehova Mulungu wako, nundipempherere, kuti dzanja langa libwerenso kwa ine. Ndipo munthuyo wa Mulungu anapembedza Yehova, ndipo dzanja la mfumu linabwezedwa kwa iye momwemo mwa kale.
Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.
Pakuti, anthu aunyinji, ndiwo ambiri a Efuremu, ndi Manase, Isakara, ndi Zebuloni, sanadziyeretse, koma anadya Paska mosati monga munalembedwa. Koma Hezekiya anawapempherera, ndi kuti, Yehova wabwino akhululukire yense
Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.
Ndipo iye adzakulankhulira iwe kwa anthu; ndipo kudzatero, kuti iye adzakhala kwa iwe ngati m'kamwa, ndi iwe udzakhala kwa iye ngati Mulungu.
Ndipo Yehova ananena ndi Mose, Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao; ndi Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako.
Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.
Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni.
Ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu, koma iwe osamchenjeza, wosanena kumchenjeza woipayo aleke njira yake yoipa, kumsunga ndi moyo, woipa yemweyo adzafa mu mphulupulu yake; koma mwazi wake ndidzaufuna padzanja lako.
Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja lako.
pamenepo padzali kuti popeza anachimwa, napalamula, azibweza zofunkha zimene analanda mwachifwamba, kapena chinthuchi adachiona ndi kusautsa mnzake, kapena choikiza anamuikiza, kapena chinthu chotayika anachipeza;
ndipo wansembeyo amchitire chomtetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa; kunena zilizonse akazichita ndi kupalamula nazo.
Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.
Ukwati uchitidwe ulemu ndi onse, ndi pogona pakhale posadetsedwa; pakuti adama ndi achigololo adzawaweruza Mulungu.
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.
Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.
Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.
Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.
Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.