Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 20:3 - Buku Lopatulika

3 Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Koma Mulungu anadza kwa Abimeleki m'kulota kwa usiku, nati kwa iye, Taona, wakufa iwe, chifukwa cha mkazi amene wamtenga: pakuti iye ndiye mkazi wa mwini.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Tsono Mulungu adamuwonekera usiku m'maloto nati, “Ufatu iwe chifukwa mkazi watengayu ndi wokwatiwa.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Koma usiku, Mulungu anafika kwa Abimeleki kutulo nati, “Ufatu iwe chifukwa cha mkazi amene watengayu popeza ndi wokwatiwa.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 20:3
22 Mawu Ofanana  

Koma Yehova anavutitsa Farao ndi banja lake ndi nthenda zazikulu chifukwa cha Sarai mkazi wake wa Abramu.


Ndipo Farao anaitana Abramu, nati, Nanga nchiyani ichi wandichitira ine? Chifukwa chanji sunandiuze ine kuti ndiye mkazi wako?


Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.


Ndipo analota, taonani, makwerero anaima pansi, pamwamba pake ndipo padafikira kumwamba: ndipo, taonani, amithenga a Mulungu analinkukwera, analinkutsika pamenepo.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Yosefe ndipo analota loto, nawafotokozera abale ake; ndipo anamuda iye koposa.


Ndipo analotanso loto lina, nafotokozera abale ake, nati, Taonani, ndalotanso loto lina: ndipo taonani, dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi khumi ndi imodzi zinandiweramira ine.


Ndipo analota maloto onse awiri, yense loto lake, usiku umodzi, yense monga mwa kumasulira kwa loto lake, wopereka chikho ndi wophika mkate wa mfumu ya Aejipito, amene anamangidwa m'kaidi.


Ndipo iwo anati kwa iye, Ife talota maloto, ndipo tilibe wotimasulira. Ndipo Yosefe anati kwa iwo, Kodi Mwini kumasulira si ndiye Mulungu? Mundifotokozeretu.


Ndipo Mulungu ananena kwa Israele, m'masomphenya a usiku, nati, Yakobo, Yakobo.


Sanalole munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa;


M'kulota, m'masomphenya a usiku, pakuwagwera anthu tulo tatikulu, pogona mwatcheru pakama,


kuti achotse munthu ku chimene akadachita, ndi kubisira munthu kudzikuza kwake;


Sanalola munthu awasautse; ndipo anadzudzula mafumu chifukwa cha iwowa.


Ndipo Yona anayamba kulowa mzindawo ulendo wa tsiku limodzi, nalalikira, nati, Atsala masiku makumi anai ndipo Ninive adzapasuka.


Ndipo Mulungu anadza kwa Balamu, nati, Anthu awa ali ndi iwe ndiwo ayani?


Koma pakusinkhasinkha iye zinthu izi, onani, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa iye m'kulota, nanena, Yosefe, mwana wa Davide, usaope kudzitengera wekha Maria mkazi wako; pakuti icho cholandiridwa mwa iye chili cha Mzimu Woyera.


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa