1 Samueli 12:19 - Buku Lopatulika19 Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201419 Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa19 Pamenepo anthu onse adauza Samuele kuti, “Chonde mutipempherere ife atumiki anu kwa Chauta, Mulungu wanu, kuti tingafe, pakuti pa machimo athu onse taonjezapo tchimo limeneli lopempha kuti tikhale ndi mfumu.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero19 Tsono anamupempha Samueli nati, “Chonde mutipempherere kwa Yehova, ife atumiki kuti tingafe pakuti pa machimo athu onse tawonjezapo tchimo lopempha mfumu.” Onani mutuwo |
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.