Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 2:17 - Buku Lopatulika

17 koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 koma mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa usadye umenewo; chifukwa tsiku lomwe udzadya umenewo udzafa ndithu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 kupatula mtengo wokhawo umene umadziŵitsa zabwino ndi zoipa. Zipatso za mtengo umenewo usadye. Ukadzadya, ndithu udzafa!”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 koma usadye zipatso za mu mtengo wodziwitsa chabwino ndi choyipa, popeza ukadzadya za mu mtengowu udzafa ndithu.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 2:17
43 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova Mulungu anameretsa m'nthaka mitengo yonse yokoma m'maso ndi yabwino kudya; ndiponso mtengo wa moyo pakati pamundapo, ndi mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa.


Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.


Ndipo anati, Ndani anakuuza iwe kuti uli wamaliseche? Kodi wadya za mtengo uja, umene ndinakuuza iwe kuti usadye?


Kwa Adamu ndipo anati, Chifukwa kuti wamvera mau a mkazi wako, nudya za mtengo umene ndinakuuza iwe kuti, Usadyeko; nthaka ikhale yotembereredwa chifukwa cha iwe; m'kusauka udzadyako masiku onse a moyo wako:


m'thukuta la nkhope yako udzadya chakudya, kufikira kuti udzabwerera kunthaka: chifukwa kuti m'menemo unatengedwa: chifukwa kuti ndiwe fumbi, ndi kufumbiko udzabwerera.


Popeza tsiku lomwelo lakutuluka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pamutu wa iwe wekha.


Ndipo mfumu inatuma munthu kukaitana Simei, niti kwa iye, Kodi sindinakulumbiritse pa Yehova ndi kukuchenjeza, kuti, Tadziwa ndithu, kuti tsiku lakutuluka iwe ndi kukayenda kwina konse udzafa ndithu? Ndipo iwe unati kwa ine, Mau amene ndawamva ndi abwino.


Ndipo panali, pamene Yeremiya anatha kunena mau onse amene Yehova anamuuza iye kuti anene kwa anthu onse, ansembe ndi aneneri ndi anthu onse anamgwira iye, ndi kuti, Udzafa ndithu.


napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira.


Pakuti sindikondwera nayo imfa ya wakufayo, ati Ambuye Yehova; chifukwa chake bwererani, nimukhale ndi moyo.


Taonani, miyoyo yonse ndi yanga, monga moyo wa atate momwemonso moyo wa mwana, ndiyo yanga; moyo wochimwawo ndiwo udzafa.


Ndipo ndikanena kwa woipa, Udzafa ndithu: koma akabwerera iye kuleka tchimo lake, nakachita choyenera ndi cholungama;


Ndikati Ine kwa woipa, Woipawe, udzafa ndithu, osanena iwe kumchenjeza woipayo aleke njira yake, woipa uyo adzafa m'mphulupulu yake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja lako.


Popeza Yehova adanena za iwowa, Adzafatu m'chipululu. Ndipo sanatsalire mmodzi wa iwowa koma Kalebe mwana wa Yefune, ndi Yoswa mwana wa Nuni.


amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.


Kodi simudziwa kuti kwa iye amene mudzipereka eni nokha kukhala akapolo ake akumvera iye, mukhalatu akapolo ake a yemweyo mulikumvera iye; kapena a uchimo kulinga kuimfa, kapena a umvero kulinga kuchilungamo?


Pakuti mphotho yake ya uchimo ndi imfa; koma mphatso yaulere ya Mulungu ndiyo moyo wosatha wa mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.


Pakuti chilamulo cha mzimu wa moyo mwa Khristu Yesu chandimasula ine ku lamulo la uchimo ndi la imfa.


Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa Khristu onse akhalitsidwa ndi moyo.


Koma mbola ya imfa ndiyo uchimo; koma mphamvu ya uchimo ndiyo chilamulo:


Pakuti onse amene atama ntchito za lamulo liwakhalira temberero; pakuti kwalembedwa, Wotembereredwa aliyense wosakhala m'zonse zolembedwa m'buku la chilamulo, kuzichita izi.


Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe.


Wotembereredwa iye wosavomereza mau a chilamulo ichi kuwachita. Ndi anthu onse anene, Amen.


Tapenyani, ndaika pamaso panu lero lino moyo ndi zokoma, imfa ndi zoipa;


Ndichititsa mboni lero, kumwamba ndi dziko lapansi zitsutse inu; ndaika pamaso panu moyo ndi imfa, mdalitso ndi temberero; potero, sankhani moyo, kuti mukhale ndi moyo, inu ndi mbeu zanu;


Ndipo inu, pokhala akufa m'zolakwa ndi kusadulidwa kwa thupi lanu, anakupatsani moyo pamodzi ndi Iye, m'mene adatikhululukira ife zolakwa zonse;


Koma iye wakutsata zomkondweretsa, adafa pokhala ali ndi moyo.


Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.


Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.


Iye wokhala nalo khutu amve chimene Mzimu anena kwa Mipingo. Iye amene apambana sadzachitidwa choipa ndi imfa yachiwiri.


Ndipo imfa ndi dziko la akufa zinaponyedwa m'nyanja yamoto. Iyo ndiyo imfa yachiwiri, ndiyo nyanja yamoto.


Wodala ndi woyera mtima ali iye amene achita nao pa kuuka koyamba; pa iwowa imfa yachiwiri ilibe ulamuliro; komatu adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu, nadzachita ufumu pamodzi ndi Iye zaka chikwizo.


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


chifukwa chake ndicho chokha chakuti adziwitse mibadwo ya ana a Israele ndi kuwaphunzitsa nkhondo, ngakhale iwo okhaokha osaidziwa konse kale;


Pakuti, pali Yehova wakupulumutsa Israele, chingakhale chili m'mwana wanga Yonatani, koma adzafa ndithu. Koma pakati pa anthu onse panalibe mmodzi wakumyankha iye.


Pamenepo Saulo anati, Mulungu andilange, naonjezereko, pakuti udzafa ndithu, Yonatani.


Popeza nthawi yonse mwana wa Yeseyo akhala ndi moyo padziko, koma sudzakhazikika iwe, kapena ufumu wako. Chifukwa chake tumiza tsopano numtengere kuno kwa ine, popeza adzafa ndithu.


Ndipo mfumu inati, Ukufa ndithu Ahimeleki, iwe ndi banja lonse la atate wako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa