Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Mafumu 5:11 - Buku Lopatulika

11 Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma Naamani adapsa mtima, nachoka, nati, Taona, ndinati m'mtima mwanga, kutuluka adzanditulukira, nadzaima ndi kuitana pa dzina la Yehova Mulungu wake, ndi kuweyula dzanja lake pamalopo, ndi kuchiritsa wakhateyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Koma Naamani atamva zimenezi, adakwiya kwambiri nachokapo. Popita iye ankati, “Ha! Ine ndimaganiza kuti atuluka kubwera pano, ndipo aimirira natama dzina la Chauta Mulungu wake mopemba, naweyula dzanja lake pamwamba pa nthendapo, ndi kundichiritsa motero.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma Naamani anachoka mokwiya ndipo anati, “Ine ndimaganiza kuti munthuyu atuluka ndipo ayimirira nayitana dzina la Yehova Mulungu wake, nayendetsa dzanja lake pamwamba pa nthendayi ndi kundichiritsa khate langa.

Onani mutuwo Koperani




2 Mafumu 5:11
19 Mawu Ofanana  

Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.


Pamenepo anamchokera, nadzitsekera yekha ndi ana ake aamuna; iwo namtengera zotengerazo, iye namatsanulira.


Ndipo Elisa anamtumira mthenga, ndi kuti, Kasambe mu Yordani kasanu ndi kawiri, ndi mnofu wako udzabwerera momwe, nudzakhala wokonzeka.


Nanga Abana ndi Faripara, mitsinje ya Damasiko, siiposa kodi madzi onse a mu Israele? Ndilekerenji kukasamba m'mwemo, ndi kukonzeka? Natembenuka, nachoka molunda.


Pakuti kubwerera m'mbuyo kwa achibwana kudzawapha; ndipo mphwai za opusa zidzawaononga.


Kudzikuza kupikisanitsa; koma omwe anauzidwa uphungu ali ndi nzeru.


Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;


Koma iye anati, Eetu, Ambuye, pakutinso tiagalu timadya nyenyeswa zakugwa pagome pa ambuye ao.


Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.


Koma kenturiyoyo anavomera nati, Ambuye, sindiyenera kuti mukalowe pansi pa tsindwi langa iai; koma mungonena mau, ndipo adzachiritsidwa mnyamata wanga.


Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.


Indetu, indetu, ndinena ndi inu, Iye wolandira aliyense amene ndimtuma, andilandira Ine; koma wolandira Ine alandira wondituma Ine.


Pamenepo Yesu anati kwa iye, Ngati simuona zizindikiro ndi zozizwa, simudzakhulupirira.


Penyani musakane wolankhulayo. Pakuti ngati iwowa sanapulumuke, pomkana Iye amene anawachenjeza padziko, koposatu sitidzapulumuka ife, odzipatulira kwa Iye wa Kumwamba;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa