Machitidwe a Atumwi 8:24 - Buku Lopatulika24 Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201424 Ndipo Simoni anayankha nati, Mundipempherere ine kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa24 Apo Simoni uja adati, “Mundipempherere inuyo kwa Ambuye kuti zimene mwanenazi zisandigwere.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero24 Ndipo Simoni anayankha, “Mundipempherere kwa Ambuye kuti zisandigwere izi mwanenazi.” Onani mutuwo |
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.