Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 27:18 - Buku Lopatulika

18 Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Koma ngati ndiwo aneneri, ndipo ngati mau a Yehova ali ndi iwo, tsopano apembedzere Yehova wa makamu, kuti zipangizo zotsala m'nyumba ya Yehova, ndi m'nyumba ya mfumu ya Yuda, ndi ku Yerusalemu, zisanke ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Ngati iwo ndi aneneridi ndipo ngati ali ndi mau a Chauta, apemphere kwa Chauta Wamphamvuzonse kuti ziŵiya zimene zidatsala m'Nyumba ya Chauta ndiponso m'nyumba ya mfumu ku Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babiloni.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 27:18
18 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anapemphera Mulungu, ndipo Mulungu anachiritsa Abimeleki, ndi mkazi wake, ndi adzakazi ake; ndipo anabala ana.


Ndipo muitane inu dzina la mulungu wanu, ine ndidzaitana dzina la Yehova; ndipo Mulunguyo ayankhe ndi moto ndiye Mulungu. Ndipo anthu onse anavomera, nati, Ndiwo mau abwino amene.


Ndipo iwo anatenga ng'ombe ija adawapatsa, naikonza, naitana dzina la Baala, kuyambira m'mawa kufikira pausana, nati, Baala, timvereni ife. Koma panalibe mau kapena wovomereza. Ndipo anavinavina kuguwa adalimanga.


Ndipo Hezekiya mfumu, ndi Yesaya mneneri mwana wa Amozi, anapemphera pa ichi, nafuulira Kumwamba.


Ndipo Yehova anati kwa ine, Ngakhale Mose ndi Samuele akadaima pamaso panga, koma mtima wanga sukadasamalira anthu awa; muwachotse iwo pamaso panga, atuluke.


Kodi choipa chibwezedwe pa chabwino? Pakuti akumbira moyo wanga dzenje. Mukumbukire kuti ndinaima pamaso panu kuwanenera zabwino, kuwachotsera iwo ukali wanu.


nati kwa Yeremiya mneneri, Chipembedzero chathu chigwe pamaso panu, nimutipempherere ife kwa Yehova Mulungu wanu, chifukwa cha otsala onsewa; pakuti tatsala ife owerengeka m'malo mwa ambiri, monga maso anu ationa ife;


Chifukwa chake iwe usapempherere anthu awa, usawakwezere iwo mfuu kapena pemphero, usandipembedze; pakuti Ine sindidzakumvera iwe.


chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.


Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.


Ndipo tsopano, mupepeze Mulungu, kuti atichitire chifundo; ichicho chichokera kwa inu; kodi Iye adzavomereza ena a inu? Ati Yehova wa makamu.


Ndipo anthu onse ananena ndi Samuele, Mupempherere akapolo anu kwa Yehova Mulungu wanu, kuti tingafe; popeza pamwamba pa zoipa zathu zonse tinaonjeza choipa ichi, chakuti tinadzipemphera mfumu.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Ndipo ana a Israele anati kwa Samuele, Musaleke kutipempherera kwa Yehova Mulungu wathu, kuti Iye atipulumutse m'manja a Afilistiwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa