Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 20:6 - Buku Lopatulika

6 Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleze iwe kuti umkhudze mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Ndipo Mulungu anati kwa iye m'kulota, Inde ndidziwa Ine, kuti wachita icho ndi mtima wangwiro, ndipo Inenso ndinakuletsa iwe kuti usandichimwire ine: chifukwa chake sindinakuloleza iwe kuti umkhudze mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Mulungu adamuyankha m'maloto momwemo kuti, “Inde ndikudziŵa kuti iwe udachita zimenezi popanda mtima wako kukutsutsa. Choncho ndidakuletsa ndine kuti usandichimwire pakumkhudza mkaziyo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Tsono kumaloto komweko Mulungu anati kwa iye, “Inde ndikudziwa kuti wachita izi moona mtima, ndipo Ine sindinafune kuti undichimwire. Nʼchifukwa chake sindinakulole kuti umukhudze.

Onani mutuwo Koperani




Genesis 20:6
22 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova anatseketsa mimba yonse ya a m'nyumba ya Abimeleki, chifukwa cha Sara mkazi wake wa Abrahamu.


Ndipo Abimeleki anauza anthu ake, nati, Aliyense amene akhudza mwamuna uyo kapena mkazi wake, zoonatu adzaphedwa.


Koma zipatso za mtengo umene uli m'kati mwa munda, Mulungu anati, Musadye umenewo, musakhudze umenewo, mungadzafe.


Ndipo Mulungu anadza kwa Labani Mwaramu usiku, nati kwa iye, Tadziyang'anira wekha, usanene kwa Yakobo kapena zabwino kapena zoipa.


Ndipo atate wanu wandinyenga ine, nasinthanitsa malipiro anga kakhumi; koma Mulungu sanamlole iye andichitire ine choipa.


Ndipo anapita ndipo kuopsa kwa Mulungu kudagwera mizinda yakuwazinga, ndipo sanalondole ana a Yakobo.


mulibe wina m'nyumba wamkulu ndine; ndipo sanandikanize ine kanthu, koma iwe, chifukwa kuti uli mkazi wake: nanga ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?


Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.


Potero ndinawaperekera kuuma mtima kwao, ayende monga mwa uphungu waowao.


Pakuti Yehova Mulungu ndiye dzuwa ndi chikopa; Yehova adzapatsa chifundo ndi ulemerero; sadzakaniza chokoma iwo akuyenda angwiro.


Pakuti ndidzaingitsa mitundu ya anthu pamaso pako, ndi kukulitsa malire ako; ndipo palibe munthu adzakhumba dziko lako, pakukwera iwe kudzaoneka pamaso pa Yehova Mulungu wako katatu chaka chimodzi.


Mtima wa mfumu uli m'dzanja la Yehova ngati mitsinje ya madzi; aulozetsa komwe afuna.


Chomwecho wolowa kwa mkazi wa mnzake; womkhudzayo sadzapulumuka chilango.


Akachimwa munthu nakachita mosakhulupirika pa Yehova nakachita monyenga ndi mnansi wake kunena za choikiza, kapena chikole, kapena chifwamba, kapena anasautsa mnansi wake;


Ndipo pamene Pilato analikukhala pa mpando wakuweruza, mkazi wake anatumiza mau kwa iye, kunena, Musachite kanthu ndi munthu wolungamayo; pakuti lero m'kulota ine ndasauka kwambiri chifukwa cha Iye.


Koma za izi munalembazi; kuli bwino kwa munthu kusakhudza mkazi.


Chifukwa chake, Tulukani pakati pao, ndipo patukani, ati Ambuye, Ndipo musakhudza kanthu kosakonzeka; ndipo Ine ndidzalandira inu,


Ndipo chifukwa chake Mulungu atumiza kwa iwo machitidwe a kusocheretsa, kuti akhulupirire bodza;


Pakuti chinsinsi cha kusaweruzika chayambadi kuchita; chokhachi pali womletsa tsopano, kufikira akamchotsa pakati.


Chifukwa chake tsono, mbuye wanga, pali Yehova, ndipo pali moyo wanu, popeza Yehova anakuletsani kuti mungakhetse mwazi, ndi kudzibwezera chilango ndi dzanja la inu nokha, chifukwa chake adani anu, ndi iwo akufuna kuchitira mbuye wanga choipa, akhale ngati Nabala.


Pakuti ndithu, Pali Yehova Mulungu wa Israele, amene anandiletsa lero kusapweteka iwe, ukadapanda kufulumira kubwera kundichingamira, zoonadi sindikadasiyira Nabala kufikira kutacha kanthu konse, ngakhale mwana wamwamuna mmodzi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa