Genesis 20:7 - Buku Lopatulika7 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Koma tsopano, umpereke mkazi ameneyu kwa mwamuna wake. Mwamunayo ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti usafe. Koma ukapanda kumpereka, ndikukuchenjezeratu kuti udzafa ndithu, iweyo ndi banja lako lonse.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Tsopano kabwezere mkaziyo kwa mwamuna wake. Iyeyu ndi mneneri, ndipo adzakupempherera kuti ukhale ndi moyo. Koma ukapanda kukamupereka, udziwiretu kuti udzafa pamodzi ndi onse a pa banja pako.” Onani mutuwo |
Ndipo tsono, mudzitengere ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri, mumuke kwa mtumiki wanga Yobu, mudzifukizire nokha nsembe yopsereza; ndi mtumiki wanga Yobu adzapempherera inu, pakuti ndidzamvomereza iyeyu, kuti ndisachite nanu monga mwa kupusa kwanu; popeza simunandinenere choyenera monga ananena mtumiki Yobu.