Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




1 Samueli 7:5 - Buku Lopatulika

5 Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Ndipo Samuele anati, Musonkhanitse Aisraele onse ku Mizipa, ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsono Samuele adati, “Sonkhanitsani mtundu wonse wa Aisraele ku Mizipa, ndipo ine ndikupemphererani kwa Chauta.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kenaka Samueli anati, “Sonkhanitsani Aisraeli onse ku Mizipa ndipo ine ndidzakupemphererani kwa Yehova.”

Onani mutuwo Koperani




1 Samueli 7:5
18 Mawu Ofanana  

Tsopano, umbwezere munthuyo mkazi wake; chifukwa iye ndiye mneneri, ndipo adzakupempherera iwe, ndipo udzakhala ndi moyo: koma ukaleka kumbwezera, udziwe kuti udzafa ndithu, iwe ndi onse amene uli nao.


ndi Mizipa, chifukwa kuti anati, Yehova ayang'anire pakati pa ine ndi iwe, pamene tisiyana wina ndi mnzake.


Ndipo pamene anamva akazembe onse a makamu, iwo ndi anthu ao, kuti mfumu ya Babiloni adaika Gedaliya wowalamulira, anadza kwa Gedaliya ku Mizipa, ndiwo Ismaele mwana wa Netaniya, ndi Yohanani mwana wa Kareya, ndi Seraya mwana wa Tanumeti wa ku Netofa, ndi Yazaniya mwana wa Mmaakati, iwo ndi anthu ao omwe.


Ndipo tsiku la makumi awiri mphambu anai la mwezi uno ana a Israele anasonkhana ndi kusala, ndi kuvala chiguduli, ndipo anali ndi fumbi.


Ndipo Yeremiya ananka kwa Gedaliya mwana wa Ahikamu ku Mizipa, nakhala kumeneko kwa anthu otsala m'dziko.


Imvani ichi, ansembe inu; mverani, inu nyumba ya Israele; tcherani khutu, inu nyumba ya mfumu; pakuti chiweruzochi chinena inu; pakuti munakhala msampha ku Mizipa, ndi ukonde woyalidwa pa Tabori.


sonkhanitsani anthu, patulani msonkhano, memezani akuluakulu, sonkhanitsani ana ndi oyamwa mawere; mkwati atuluke m'chipinda mwake, ndi mkwatibwi m'mogona mwake.


ndi Dileani, ndi Mizipa, ndi Yokotele;


ndi Mizipa, ndi Kefira, ndi Moza;


Ndipo ana a Amoni analalikiridwa, namanga misasa mu Giliyadi. Ndi ana a Israele anasonkhana namanga misasa ku Mizipa.


Pamenepo anatuluka ana onse a Israele, nuunjikana msonkhano kwa Yehova ku Mizipa ngati munthu mmodzi, kuyambira ku Dani mpaka Beereseba ndi dziko la Giliyadi lomwe.


Ndipo Samuele anaitana anthu onse asonkhane kwa Yehova ku Mizipa;


Si nyengo yakumweta tirigu lero kodi? Ndidzaitana kwa Yehova, kuti atumize bingu ndi mvula; ndipo mudzazindikira ndi kuona kuti choipa chanu munachichita pamaso pa Yehova ndi kudzipemphera mfumu, nchachikulu.


Ndipo inenso, kukhale kutali ndi ine, kuchimwira Yehova ndi kuleka kukupemphererani; koma ndidzakulangizani njira yabwino ndi yolungama.


Pamenepo Samuele anatenga mwala nauimika pakati pa Mizipa ndi Sene, nautcha dzina lake Ebenezeri, nati, Kufikira pano Yehova anatithandiza.


Ndipo anayenda chozungulira chaka ndi chaka ku Betele, ndi ku Giligala, ndi ku Mizipa; naweruza Israele m'malo onse amenewa.


Pomwepo ana a Israele anachotsa Abaala ndi Asitaroti, natumikira Yehova yekha.


Koma chimenechi sichinakondweretse Samuele, pamene iwo anati, Tipatseni mfumu kuti itiweruze. Ndipo Samuele anapemphera kwa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa