1 Samueli 7:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele mu Mizipa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo anaunjikana ku Mizipa, natunga madzi, nawatsanula pamaso pa Yehova, nasala chakudya tsiku lija, nati, Tinachimwira Yehova. Ndipo Samuele anaweruza ana a Israele m'Mizipa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Choncho adasonkhana ku Mizipa, natunga madzi ndi kuŵathira pansi pamaso pa Chauta mopepesera, ndipo adasala chakudya tsiku limenelo, namanena kuti, “Tidachimwira Chauta.” Nku Mizipako kumene Samuele ankaweruza milandu ya Aisraele. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Choncho anasonkhana ku Mizipa, ndipo anatunga madzi ndi kuwathira pansi pamaso pa Yehova. Pa tsiku limenelo anasala kudya namanena kuti, “Ife tachimwira Yehova.” Ndipo Samueli anali mtsogoleri wa Israeli ku Mizipa. Onani mutuwo |