Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Eksodo 18:21 - Buku Lopatulika

Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna amtima, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makhumi;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Koma sankhani amuna odziwa ntchito yawo, anthu owopa Mulungu, anthu odalirika amene amadana ndi kupeza phindu mwachinyengo. Tsono muwayike kuti akhale oyangʼanira anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50 ndi ena a anthu khumi.

Onani mutuwo



Eksodo 18:21
49 Mawu Ofanana  

Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


dziko la Ejipito lili pamaso pako: uwakhazike atate wako ndi abale ako pa dera lokometsetsa la dziko; akhale m'dziko la Goseni; ndipo ngati udziwa anthu anzeru a mwa iwo, uwaike iwo ayang'anire ng'ombe zanga.


Ndipo Davide anawerenga anthu amene anali naye, nawaikira atsogoleri a zikwi ndi atsogoleri a mazana.


Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.


Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.


Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;


Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.


Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?


ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.


Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Ndinali atate wa waumphawi; ndi mlandu wa iye amene sindinamdziwe ndinafunsitsa.


Ngati ndapeputsa mlandu wa kapolo wanga, kapena wa mdzakazi wanga, potsutsana nane iwo,


Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?


Ndalama zake sakongoletsa mofuna phindu lalikulu, ndipo salandira chokometsera mlandu kutsutsa wosachimwa. Munthu wakuchita izi sadzagwedezeka kunthawi zonse.


Ndipo Mose anati kwa Yoswa, Utisankhulire amuna, nutuluke kuyambana naye Amaleke; mawa ndidzaima pamwamba pa chitunda, ndi ndodo ya Mulungu m'dzanja langa.


Ndipo Mose anasankha amuna anzeru mwa Aisraele onse, nawaika akulu a pa anthu, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, ndi akulu a pa makumi.


Pochimwa dziko akalonga ake achuluka; koma anthu ozindikira ndi odziwa alikhazikikitsa nthawi yaikulu.


Mau atha; zonse zamveka zatha; opa Mulungu, musunge malamulo ake; pakuti choyenera anthu onse ndi ichi.


Ndipo mpando wachifumu udzakhazikika m'chifundo, ndimo wina adzakhala pamenepo m'zoona, m'chihema cha Davide, nadzaweruza, nadzafunitsa chiweruziro, nadzafulumira kuchita chilungamo.


Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;


Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


wosapereka molira phindu, wosatenga choonjezerapo wobweza dzanja lake lisachite chosalungama, woweruza zoona pakati pa munthu ndi mnzake,


Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.


Watero Yehova wa makamu, kuti, Weruzani chiweruzo choona, nimuchitire yense mnzake chifundo ndi ukoma mtima;


Izi ndizo muzichite: Nenani choonadi yense ndi mnzake; weruzani zoona ndi chiweruzo cha mtendere m'zipata zanu;


Iwo ndiwo oitanidwa a khamu, akalonga a mafuko a makolo ao; ndiwo akulu a zikwizo za Israele.


Ndipo pamodzi ndi inu pakhale munthu mmodzi wa mafuko onse; yense mkulu wa nyumba ya kholo lake.


Akaliza limodzi, pamenepo akalonga, akulu a zikwi a mu Israele, azisonkhana kuli iwe.


nanena, M'mzinda mwakuti munali woweruza wosaopa Mulungu, ndi wosasamala munthu.


Ndipo sanafune nthawi; koma bwinobwino anati mwa yekha, Ndingakhale sindiopa Mulungu kapena kusamala munthu;


Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense.


Chifukwa chake, abale, yang'anani mwa inu amuna asanu ndi awiri a mbiri yabwino, odzala ndi Mzimu ndi nzeru, amene tikawaike asunge ntchito iyi.


Pamenepo akulu a mzindawo azitenga munthuyu ndi kumkwapula;


wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;


ndi akalonga khumi naye; nyumba imodzi ya atate kalonga mmodzi, kotero ndi mafuko onse a Israele; yense wa iwowa ndiye mkulu wa nyumba ya atate ao mwa mabanja a Israele.


idzawaika akhale otsogolera chikwi, ndi otsogolera makumi asanu; ndipo idzaika ena kulima minda yake, ndi kutema dzinthu zake, ndi kumpangira zipangizo za nkhondo, ndi zipangizo za magaleta.


Ndipo ana ake sanatsanze makhalidwe ake, koma anapatukira ku chisiriro, nalandira chokometsera mlandu, naipitsa kuweruza.