Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 7:2 - Buku Lopatulika

2 ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 ndipo ndinawapatsa mbale wanga Hanani, ndi Hananiya kazembe wa kuboma, ulamuliro wa pa Yerusalemu; popeza ndiye munthu wokhulupirika, naposa ambiri pakuopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Pamenepo ndidasankha mbale wanga Hanani ndi Hananiya, mkulu woyang'anira linga lankhondo, kuti aŵiriwo azilamulira Yerusalemu. Hananiyayo anali munthu wokhulupirika ndi womvera Mulungu kupambana anthu ambiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Kenaka ine ndinasankha mʼbale wanga Hanani pamodzi ndi Hananiya woyangʼanira nsanja yankhondo kukhala olamulira Yerusalemu chifukwa iyeyu anali munthu odalirika ndi woopa Mulungu kuposa anthu ena.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:2
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Mulungu wa Israele anati, Thanthwe la Israele linalankhula ndi ine; kudzakhala woweruza anthu molungama; woweruza m'kuopa Mulungu.


Ndipo kudzachitika, ine ntakusiyani, mzimu wa Yehova udzakunyamulirani kosakudziwa ine, ndipo ine ntakauza Ahabu, ndipo akalephera kukupezani, adzandipha. Koma ine kapolo wanu ndimaopa Yehova kuyambira ubwana anga.


Ndipo Ahabu anaitana Obadiya woyang'anira nyumba yake. Koma Obadiya anaopa ndithu Yehova;


anafika Hanani, mmodzi wa abale anga, iye ndi amuna ena a ku Yuda; ndipo ndinawafunsa za Ayuda adapulumukawo otsala andende, ndi za Yerusalemu.


Hoseya, Hananiya, Hasubu,


Ndinaikanso osunga chuma, asunge nyumba za chuma: Selemiya wansembe, ndi Zadoki mlembi; ndi wa Alevi, Pedaya; ndi wakuwathandiza, Hanani mwana wa Zakuri, mwana wa Mataniya; popeza anayesedwa okhulupirika ndi udindo wao, ndiwo kugawira abale ao.


ndi kalata kwa Asafu wosunga misitu ya mfumu, kuti andipatse mitengo ya mitanda ya kuzipata za linga lili ku Kachisi, ndi ya linga la mzinda, ndi ya nyumba imene ndidzalowamo ine. Ndipo mfumu inandipatsa monga mwa dzanja lokoma la Mulungu londikhalira.


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Ndinanenanso nao, Asatsegule pa zipata za Yerusalemu lisanafunde dzuwa; ndi poimirira odikira atseke pazipata, nimuzipiringidze, nimuike alonda mwa iwo okhala mu Yerusalemu, yense polindirira pake, yense pandunji pa nyumba yake.


Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Maso anga ayang'ana okhulupirika m'dziko, kuti akhale ndi Ine; iye amene ayenda m'njira yangwiro, iyeyu adzanditumikira Ine.


Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;


Ndipo akuluwa ndi akalonga anayesa kumtola chifukwa Daniele, kunena za ufumuwo; koma sanakhoze kupeza chifukwa kapena cholakwira, popeza anali wokhulupirika; ndipo saonana chosasamala kapena cholakwa chilichonse mwa iye.


Satero mtumiki wanga Mose; ndiye wokhulupirika m'nyumba mwanga monse.


Ndani kodi ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, amene mbuye wake anamkhazika woyang'anira banja lake, kuwapatsa zakudya pa nthawi yake?


Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako.


Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.


Ndipo zimene wazimva kwa ine mwa mboni zambiri, zomwezi uikize kwa anthu okhulupirika, amene adzadziwa kuphunzitsa enanso.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa