Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 7:1 - Buku Lopatulika

1 Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Ndipo atatha kumanga linga, ndinaika zitseko, nakhazika odikira, ndi oimbira, ndi Alevi;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Khoma la mzinda lija litamangidwa, ndidaikira zitseko, ndipo alonda a ku Nyumba ya Mulungu, anthu oimba nyimbo ndiponso Alevi adasankhidwa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Khoma linamangidwa ndipo zitseko zinayikidwa. Pambuyo pake alonda a Nyumba ya Mulungu, oyimba nyimbo ndiponso Alevi anasankhidwa.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 7:1
12 Mawu Ofanana  

Nadza iwo, naitana mlonda wa mzinda, namfotokozera; ndi kuti, Tinafika ku misasa ya Aaramu, ndipo taonani, palibe munthu pomwepo, kapena mau a munthu, koma akavalo omanga, ndi abulu omanga, ndi mahema ali chimangire.


Ndipo Hezekiya anaika zigawo za ansembe ndi Alevi, monga mwa magawidwe ao, yense monga mwa utumiki wake, ndi ansembe ndi Alevi, achite nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika kutumikira, ndi kuyamika, ndi kulemekeza, kuzipata za chigono cha Yehova.


Chaka chachiwiri tsono chakufika iwo kunyumba ya Mulungu ku Yerusalemu, mwezi wachiwiri, Zerubabele mwana wa Sealatiele, ndi Yesuwa mwana wa Yozadaki, ndi abale ao otsala, ansembe ndi Alevi, ndi onse ochokera kundende kudza ku Yerusalemu, anayamba, naika Alevi a zaka makumi awiri ndi mphambu, ayang'anire ntchito ya nyumba ya Yehova.


Pakuti ana a Israele ndi ana a Levi, azibwera nayo nsembe yokweza yatirigu, ndi yavinyo ndi yamafuta, kuzipinda kuli zipangizo za malo opatulika, ndi ansembe akutumikira, ndi odikira, ndi oimbira; kuti tisasiye nyumba ya Mulungu wathu.


Awa tsono ndi akulu a dziko okhala mu Yerusalemu; koma m'midzi ya Yuda yense anakhala pa cholowa chake m'midzi mwao, ndiwo Israele, ansembe, ndi Alevi, ndi antchito a m'kachisi, ndi ana a akapolo a Solomoni.


Ndi akulu a Alevi: Hasabiya, Serebiya, ndi Yesuwa mwana wa Kadimiyele, ndi abale ao openyana nao, kulemekeza ndi kuyamika, monga mwa lamulo la Davide munthu wa Mulungu, alonda kupenyana alonda.


Kunali tsono, atamva Sanibalati, ndi Tobiya, ndi Gesemu Mwarabu, ndi adani athu otsala, kuti ndidatha kumanga lingali, posatsalaponso popasuka; (ngakhale pajapo sindinaike zitseko pazipata);


Ndipo linga linatsirizika pa tsiku la makumi awiri ndi lachisanu la mwezi wa Eluli, titalimanga masiku makumi asanu mphambu awiri.


Anatchulanso ntchito zake zokoma pamaso panga namfotokozera iye mau anga. Ndipo Tobiya anatumiza makalata kuti andiopse ine.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa