Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 5:1 - Buku Lopatulika

1 Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 “Thamangani uku ndi uku m'miseu ya Yerusalemu, mudziwonere nokha. Funafunani ku mabwalo ake ngati mungapezeke munthu, munthu wake wochita zolungama, wofunitsitsa zoona, kuti choncho Yerusalemu ndidzamkhululukire.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 “Pitani uku ndi uku mʼmisewu ya Yerusalemu, mudzionere nokha, funafunani mʼmabwalo ake. Ngati mungapeze munthu mmodzi amene amachita zachilungamo ndi kufunafuna choonadi, ndipo ndidzakhululukira mzinda uno.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 5:1
29 Mawu Ofanana  

Ndipo anati, Ine ndinachitira changu Yehova Mulungu wa makamu; popeza ana a Israele anasiya chipangano chanu, napasula maguwa anu a nsembe, napha aneneri anu ndi lupanga, ndipo ndatsala ndekha, ndipo afuna moyo wanga kuuchotsa.


Pakuti maso a Yehova ayang'ana uko ndi uko m'dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wao uli wangwiro ndi Iye. Mwachita chopusa m'menemo; pakuti kuyambira tsopano mudzaona nkhondo.


Pulumutsani, Yehova; pakuti wofatsa wasowa; pakuti okhulupirika achepa mwa ana a anthu.


Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.


Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.


Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake?


Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?


Gula ntheradi, osaigulitsa; nzeru, ndi mwambo, ndi luntha.


pambali pa chipata polowera m'mudzi, polowa anthu pa makomo ifuula:


Ndinati, Ndiuketu, ndiyendeyende m'mzinda, m'makwalala ndi m'mabwalo ake, ndimfunefune amene moyo wanga umkonda: Ndimfunafuna, koma osampeza.


Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.


Chifukwa chanji mudzatsutsana ndi Ine nonse? Mwandilakwira Ine, ati Yehova.


Ndipo amuna onse amene anadziwa kuti akazi ao anafukizira milungu ina, ndi akazi onse omwe anaimirirapo, msonkhano waukulu, anthu onse okhala m'dziko la Ejipito, mu Patirosi, anamyankha Yeremiya, kuti,


Ndinatchera khutu, ndinamva koma sananene bwino; panalibe munthu amene anatembenuka kusiya zoipa zake, ndi kuti, Ndachita chiyani? Yense anatembenukira njira yake, monga akavalo athamangira m'nkhondo.


Ha, ndikadakhala ndi chigono cha anthu aulendo m'chipululu; kuti ndisiye anthu anga, ndiwachokere, pakuti onse ali achigololo, msonkhano wa anthu achiwembu.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?


Ndipo ndinafunafuna munthu pakati pao wakumanganso linga, ndi kuimira dziko popasukira pamaso panga, kuti ndisaliononge; koma ndinapeza palibe.


Pamenepo ananena nane, Mphulupulu ya nyumba ya Israele ndi Yuda ndi yaikulukulu ndithu, ndi dziko ladzala ndi mwazi, ndi mzindawo wadzala ndi kukhotetsa milandu; pakuti ati, Yehova wataya dziko, Yehova sapenya.


Koma iwe Daniele, tsekera mau awa, nukomere chizindikiro buku, mpaka nthawi ya chimaliziro; ambiri adzathamanga chauko ndi chauko, ndi chidziwitso chidzachuluka.


Alumphira mzinda, athamanga palinga, akwerera nyumba, alowera pamazenera ngati khungu.


Ndipo adzayendayenda peyupeyu kuyambira kunyanja kufikira kunyanja ndi kuyambira kumpoto kufikira kum'mawa; adzathamangathamanga kufunafuna mau a Yehova, koma osawapeza.


nanena naye, Thamanga, lankhula ndi mnyamata uyu, ndi kuti, Mu Yerusalemu mudzakhala anthu ngati m'midzi yopanda malinga, chifukwa cha kuchuluka anthu ndi zoweta momwemo.


Ndipo kapoloyo pakubwera anauza mbuye wake zinthu izi. Pamenepo mwini nyumba anakwiya, nati kwa kapolo wake, Tuluka msanga, pita kumakwalala ndi kunjira za mzinda, nubwere nao muno aumphawi ndi opunduka ndi akhungu ndi otsimphina.


ndi m'chinyengo chonse cha chosalungama kwa iwo akuonongeka, popeza chikondi cha choonadi sanachilandire, kuti akapulumutsidwe iwo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa