Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 4:31 - Buku Lopatulika

31 Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Pakuti ndamva kubuula ngati kwa mkazi wobala, ndi msauko ngati wa mkazi wobala mwana wake woyamba, mau a mwana wamkazi wa Ziyoni wakupuma mosiyiza, wakutambasula manja ake, ndi kuti, Tsoka ine tsopano! Pakuti moyo wanga walefuka chifukwa cha ambanda.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Ndidamva kulira ngati kwa mkazi pa nthaŵi yake yochira, kubuula ngati kwa mkazi pa uchembere wake woyamba. Kumeneku kunali kulira kwa anthu a mu Ziyoni, ŵefuŵefu, atatambalitsa manja ao, akunena kuti, “Tsoka ife! Tikukomoka, moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Ndikumva kulira ngati kwa mayi pa nthawi yake yobereka, kubuwula ngati kwa mayi amene akubereka mwana wake woyamba. Kuliraku ndi kwa anthu a mu Ziyoni, wefuwefu. Atambalitsa manja awo nʼkumati, “Kalanga ife! Tikukomoka. Moyo wathu waperekedwa kwa anthu otipha.”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 4:31
35 Mawu Ofanana  

Ndipo anati Rebeka kwa Isaki, Ndalema moyo wanga chifukwa cha ana aakazi a Ahiti, akatenga Yakobo mkazi wa ana aakazi a Ahiti, onga ana aakazi a m'dziko lino, moyo wanga udzandikhalira ine bwanji?


Mtima wanga ulema nao moyo wanga, ndidzadzilolera kudandaula kwanga, ndidzalankhula pakuwawa mtima wanga.


Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!


Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.


ndipo adzaopa; zowawa ndi masauko zidzawagwira; ndipo adzamva zowawa, ngati mkazi wakubala; adzazizwa wina ndi wina; nkhope zao zidzanga malawi a moto.


Chifukwa chake m'chuuno mwanga mwadzazidwa ndi zopota; zopweteka zandigwira ine monga zopweteka za mkazi pobala mwana; zowawa zindiweramitsa, makutu anga sangathe kumva; ndichita mantha sindingathe kuona.


Monga ngati mkazi wokhala ndi pakati, amene nthawi yake yakubala yayandikira, amva zopweteka, ndi kufuula m'zowawa zake; momwemo takhala ife pamaso panu, Yehova.


Ndakhala nthawi yambiri wosalankhula ndakhala chete kudzithungata ndekha; tsopano ndidzafuula ngati mkazi wobala; ndidzapuma modukizadukiza ndi wefuwefu pamodzi.


Ndipo ine ndinati, Tsoka kwa ine! Chifukwa ndathedwa; chifukwa ndili munthu wa milomo yonyansa, ndikhala pakati pa anthu a milomo yonyansa; chifukwa kuti maso anga aona Mfumu, Yehova wa makamu.


Tsoka ine, ndalaswa! Bala langa lindipweteka; koma ine ndinati, Ndithu vuto langa ndi ili, ndipirire nalo.


Udzanena chiyani pamene adzaika abale ako kukhala akulu ako, pakuti iwe wekha wawalangiza iwo akukana iwe? Kodi zowawa sizidzakugwira iwe monga mkazi wobala?


Ndikatulukira kumunda, taonani ophedwa ndi lupanga! Ndikalowa m'mzinda, taonani odwala ndi njala! Pakuti mneneri ndi wansembe ayendayenda m'dziko osadziwa kanthu.


Kupweteka kwanga kuli chipwetekere bwanji, ndi bala langa losapoleka, likana kupola? Kodi mudzakhala kwa ine ngati kamtsinje konyenga, ngati madzi omwerera?


Chifukwa chake mupereke ana ao kunjala, mupereke iwo kumphamvu ya lupanga; akazi ao akhale opanda ana, ndi amasiye; amuna ao aphedwe ndi imfa, ndi anyamata ao apandidwe ndi lupanga kunkhondo.


Iwe wokhala mu Lebanoni, womanga chisa chako m'mikungudza, udzachitidwa chisoni chachikulu nanga pamene mapweteko adzadza kwa iwe, monga mkazi alinkudwala!


Funsani tsopano, ndi kuona ngati mwamuna aona mwana; chifukwa chanji ndiona mwamuna ndi manja ake pa chuuno chake, monga mkazi alinkubala, ndi nkhope zao zotumbuluka?


Yehova Mulungu wa Israele atero kwa inu, Baruki:


Keriyoti walandidwa, ndi malinga agwidwa, ndipo tsiku lomwelo mtima wa anthu amphamvu a Mowabu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Taonani, adzafika nadzauluka ngati chiombankhanga, adzatambasulira Bozira mapiko ake, ndipo tsiku lomwemo mtima wa anthu amphamvu a Edomu adzakhala ngati mtima wa mkazi alinkudwala.


Damasiko walefuka, atembenukira kuti athawe, kunthunthumira kwamgwira; zovuta ndi kulira zamgwira iye, ngati mkazi alimkudwala.


Mfumu ya ku Babiloni yamva mbiri yao, ndipo manja ake alefuka; wagwidwa ndi nkhawa, ndi zowawa zonga za mkazi alimkudwala.


Ndidzachotsa mwana wamkazi wa Ziyoni mkazi wokoma ndi wololopoka.


Ziyoni atambasula manja ake, palibe wakumtonthoza; Yehova walamulira kuti omzungulira Yakobo akhale adani ake; Yerusalemu wasanduka chinthu chonyansa pakati pao.


Onani, Yehova; pakuti ndavutika, m'kati mwanga mugwedezeka; mtima wanga wasanduka mwa ine; pakuti ndapikisana nanu ndithu; kunjako lupanga limangopha ana; m'nyumba muli imfa.


Wamng'ono ndi nkhalamba agona pansi m'makwalala; anamwali ndi anyamata anga agwa ndi lupanga; munawapha tsiku la mkwiyo wanu, munawagwaza osachitira chisoni.


Zowawa zonga za mkazi wobala zidzamgwera, ndiye mwana wopanda nzeru; pakuti pali nyengo yakuti asachedwe mobalira ana.


Imva zowawa, nuyesetse kubala, mwana wamkazi wa Ziyoni, ngati mkazi wakubala; pakuti udzatuluka m'mzinda tsopano, nudzakhala kuthengo, nudzafika ku Babiloni; komweko udzapulumutsidwa; komweko Yehova adzakuombola m'manja a adani ako.


Tsono ufuulitsa chifukwa ninji? Palibe mfumu mwa iwe kodi? Watayika kodi mu uphungu wako, kuti zowawa zakugwira ngati mkazi wobala?


Kalanga ine! Pakuti ndikunga atapulula zipatso za m'mwamvu, atakunkha m'munda wampesa; palibe mphesa zakudya; moyo wanga ukhumba nkhuyu yoyamba kupsa.


Tauzani mwana wamkazi wa Ziyoni, Taona, mfumu yako idza kwa iwe, wofatsa ndi wokwera pabulu, ndi pa kabulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.


Pakuti ngati ndilalikira Uthenga Wabwino ndilibe kanthu kakudzitamandira; pakuti chondikakamiza ndigwidwa nacho; pakuti tsoka ine ngati sindilalikira Uthenga Wabwino.


Pamene angonena, Mtendere ndi mosatekeseka, pamenepo chionongeko chobukapo chidzawagwera, monga zowawa mkazi wa pakati; ndipo sadzapulumuka konse.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa