Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 18:22 - Buku Lopatulika

22 ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

22 ndipo iwo aweruze milandu ya anthu nthawi zonse; ndipo kudzakhala kuti milandu yaikulu yonse abwere nayo kwa iwe; koma milandu yaing'ono yonse aweruze okha; potero idzakuchepera ntchito, ndi iwo adzasenza nawe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

22 Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

22 Tsono amenewa aziweruza anthu nthawi zonse. Mlandu uliwonse waukulu azibwera nawo kwa inu, koma mlandu waungʼono aziweruza okha. Izi zidzachititsa kuti ntchito yanu ipepuke, popeza mudzagwira ntchito mothandizana.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 18:22
12 Mawu Ofanana  

Ndipo iwe Ezara monga mwa nzeru za Mulungu wako ili m'dzanja lako, uike nduna, ndi oweruza milandu, aweruze anthu onse ali tsidya lija la mtsinje, onse akudziwa malamulo a Mulungu wako; ndi wosawadziwayo umphunzitse.


Udzalema konse, iwe ndi anthu amene uli nao; pakuti chikukanika chinthu ichi; sungathe kuchichita pa wekha.


Ukachite chinthuchi, ndi Mulungu akakuuza chotero, udzakhoza kupirira, ndi anthu awa onse adzapita kwao mumtendere.


Ndipo anaweruza anthu nthawi zonse; mlandu wakuwakanika amabwera nao kwa Mose, ndi milandu yaing'ono yonse amaweruza okha.


ndipo mwana wamwamuna wa mkazi Wachiisraele anachitira Dzina mwano, natemberera; ndipo anadza naye kwa Mose. Dzina la mai wake ndiye Selomiti, mwana wa Dibiri, wa fuko la Dani.


Pamenepo ndidzatsika ndi kulankhula nawe komweko; ndipo ndidzatengako mzimu uli pa iwe, ndi kuika pa iwowa; adzakuthandiza kusenza katundu wa anthu awa, kuti usasenze wekha.


Ndipo amene adampezawo alinkufuna nkhuni anabwera naye kwa Mose ndi Aroni, ndi kwa khamu lonse.


Ndipo anaima pamaso pa Mose, ndi pamaso pa Eleazara wansembe, ndi pamaso pa akalonga; ndi khamu lonse, pakhomo pa chihema chokomanako, ndi kuti,


Ndipo akulu a makolo a mabanja a ana a Giliyadi, mwana wa Makiri, mwana wa Manase, wa mabanja a ana a Yosefe, anayandikiza, nanena pamaso pa Mose, ndi pamaso pa akalonga, ndiwo akulu a makolo a ana a Israele;


Pakuti chifukwa cha ichi mupatsanso msonkho; pakuti iwo ndiwo atumiki a Mulungu akulabadirabe chinthu chimenechi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa