Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 5:9 - Buku Lopatulika

9 Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Tsono ine ndidaonjeza kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwinotu ai. Muziwopa Mulungu ndi kumachita zolungama, kuti adani athu a mitundu inaŵa asapeze chifukwa chotinyozera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kotero ndinapitiriza kunena kuti, “Zimene mukuchitazi si zabwino. Kodi inu simungakhale ndi moyo woopa Mulungu wathu kuti tipewe kunyoza kwa adani athu, anthu a mitunda inayi?

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 5:9
21 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.


Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere chitonzo chao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale chofunkhidwa m'dziko la ndende;


Kodi ine, ndi abale anga, ndi anyamata anga, tiwakongoletsa ndalama ndi tirigu mwa phindu? Ndikupemphani, tileke phindu ili.


Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.


Adziwa mphamvu ya mkwiyo wanu ndani, ndi ukali wanu monga ayenera kukuopani?


Munthu wa chiwawa akopa mnzake, namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.


Kulipiritsa wolungama sikuli kwabwino, ngakhale kukwapula akulu chifukwa aongoka mtima.


Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino, ngakhale kuchitira chetera wolungama.


Kukhumba kosadziwa sikuli kwabwino; ndipo wofulumira ndi mapazi ake amachimwa.


Izinso zili za anzeru, poweruza chetera silili labwino.


Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m'dziko mwake.


Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe.


Pamenepo ndipo Mpingo wa mu Yudeya yense ndi Galileya ndi Samariya unali nao mtendere, nukhazikika; ndipo unayenda m'kuopa kwa Ambuye ndi m'chitonthozo cha Mzimu Woyera, nuchuluka.


Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.


Chifukwa chake nditi akwatiwe amasiye aang'ono, nabale ana, naweruzire nyumba, osapatsa chifukwa kwa mdaniyo chakulalatira;


akhale odziletsa, odekha, ochita m'nyumba mwao, okoma, akumvera amuna a iwo okha, kuti mau a Mulungu angachitidwe mwano.


ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.


Iai, ana anga, popeza mbiri imene ndilikuimva sili yabwino iai; mulikulakwitsa anthu a Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa