Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yobu 1:1 - Buku Lopatulika

1 Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Panali munthu m'dziko la Uzi, dzina lake ndiye Yobu; ndipo munthuyu anali wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Kudaali munthu wina, dzina lake Yobe, amene ankakhala m'dziko la Uzi. Munthu ameneyo anali wosalakwa ndiponso wolungama. Ankaopa Mulungu namapewa zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mʼdziko la Uzi munali munthu wina, dzina lake Yobu. Munthu ameneyu anali wosalakwa ndi wolungama mtima, ankaopa Mulungu ndi kupewa zoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Yobu 1:1
34 Mawu Ofanana  

Ndi ana a Aramu: Uzi ndi Huli ndi Getere, ndi Masi.


Pamene Abramu anali wa zaka makumi asanu ndi anai kudza zisanu ndi zinai, Yehova anamuonekera Abramu nati kwa iye, Ine ndine Mulungu Wamphamvuyonse; yenda iwe pamaso panga, nukhale wangwiro.


Ndipo mthenga anati, Usaike dzanja lako pa mwana, usamchitire iye kanthu; chifukwa tsopano ndidziwa kuti iwe umuopa Mulungu wako, pakuti sunandikanize ine mwana wako, mwana wako wayekha.


Ana a Disani ndi awa: Uzi ndi Arani.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Mibadwo ya Nowa ndi iyi: Nowa anali munthu wolungama ndi wangwiro m'mibadwo yake; Nowa anayendabe ndi Mulungu.


Mukumbukire Yehova kuti ndinayendabe pamaso panu m'choonadi, ndi mtima wangwiro, ndi kuchita zokoma m'kuona kwanu. Nalira Hezekiya kulira kwakukulu.


Ana a Semu: Elamu, ndi Asiriya, ndi Aripakisadi, ndi Ludi, ndi Aramu, ndi Uzi, ndi Huli, ndi Getere, ndi Meseki.


Ana a Ezere: Bilihani, ndi Zaavani, ndi Yaakani. Ana a Disani: Uzi, ndi Arani.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupewa zoipa.


Ndipo Yehova anati kwa Satana, Kodi waonerera mtumiki wanga Yobu? Pakuti palibe wina wonga iye m'dzikomo, munthu wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu, ndi kupewa zoipa; naumirirabe kukhala wangwiro, chinkana undisonkhezera ndimuononge kopanda chifukwa.


Koma kwa munthu anati, Taonani, kuopa Ambuye ndiko nzeru; ndi kupatukana nacho choipa ndiko luntha.


Kodi kulimbika mtima kwako si ndiko kuti uopa Mulungu, ndi chiyembekezo chako si ndiwo ungwiro wa njira zako?


Chinkana ndikhala wangwiro, sindidzisamalira mwini, ndipeputsa moyo wanga.


Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;


Wanzeru amaopa nasiya zoipa; koma wopusa amanyada osatekeseka.


Woyenda moongoka mtima aopa Yehova; koma wokhota m'njira yake amnyoza.


Khwalala la oongoka mtima ndilo lakuti asiye zoipa; wosunga njira yake atchinjiriza moyo wake.


Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.


Wolungama woyenda mwangwiro, anake adala pambuyo pake.


Usadziyese wekha wanzeru; opa Yehova, nupatuke pazoipa;


Kuopa Yehova ndiko kuda zoipa; kunyada, ndi kudzikuza, ndi njira yoipa, ndi m'kamwa mokhota, ndizida.


ndi anthu onse osakanizidwa, ndi mafumu onse a dziko la Uzi, ndi mafumu onse a dziko la Afilisti, ndi Asikeloni, ndi Gaza, ndi Ekeroni, ndi otsala a Asidodi,


kondwera nusangalale, mwana wamkazi wa Edomu, wokhala m'dziko la Uzi; chikho chidzapita ngakhale mwa iwenso; udzaledzera ndi kuvula zako.


chinkana akadakhala m'mwemo anthu awa atatu, Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadapulumutsa moyo wao wokha mwa chilungamo chao, ati Ambuye Yehova.


chinkana Nowa, Daniele, ndi Yobu, akadakhala m'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, sakadapulumutsa ana aamuna kapena aakazi; akadapulumutsa moyo wao wokha ndi chilungamo chao.


Ndipo onse awiri anali olungama mtima pamaso pa Mulungu, namayendabe m'malamulo onse ndi zoikika za Ambuye osachimwa.


Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.


Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo.


ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa