Eksodo 13:14 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;
Onani mutuwo
Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo, ndi dzanja lamphamvu;
Onani mutuwo
M'tsogolo mwana wanu wamwamuna adzakufunsani kuti, ‘Kodi zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Pamenepo inu mudzayankhe kuti, ‘Chauta adatitulutsa ku Ejipito, ku dziko laukapolo, ndi dzanja lake lamphamvu.
Onani mutuwo
“Mʼtsogolomo mwana wanu akakafunsa kuti, ‘Zimenezi zikutanthauza chiyani?’ Mukamuwuze kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo ndi dzanja lamphamvu.
Onani mutuwo