Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Danieli 9:15 - Buku Lopatulika

15 Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 “Inu Ambuye Mulungu wathu, munatulutsa anthu anu ku Igupto ndi dzanja lanu lamphamvu ndipo dzina lanu ndi lotchuka mpaka lero. Ife tachimwa, tachita zolakwa.

Onani mutuwo Koperani




Danieli 9:15
30 Mawu Ofanana  

pakuti awa ndi anthu anu ndithu, ndi cholowa chanu chimene munatulutsa mu Ejipito, m'kati mwa ng'anjo ya chitsulo;


popeza anachita choipa pamaso panga, nautsa mkwiyo wanga chitulukire makolo ao mu Ejipito, mpaka lero lino.


koma akalingirira m'mtima mwao kudziko kumene anawatengera andende, nakatembenuka, nakapembedzera Inu m'dziko la undende wao, ndi kuti, Tachimwa, tachita mphulupulu, tachita choipa;


Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikulu, ndi dzanja lanu lolimba.


mutchere khutu, ndi maso anu atseguke kumvera pemphero la kapolo wanu, ndilipempha pamaso panu tsopano apa msana ndi usiku, kupempherera ana a Israele akapolo anu, ndi kuwulula zoipa za ana a Israele zimene tachimwira nazo Inu; inde tachimwa, ine ndi nyumba ya atate wanga.


nimunachitira zizindikiro ndi zodabwitsa Farao ndi akapolo ake onse, ndi anthu onse a m'dziko lake; popeza munadziwa kuti anawachitira modzikuza; ndipo munadzibukitsira dzina monga lero lino.


Koma anawapulumutsa chifukwa cha dzina lake, kuti adziwitse chimphamvu chake.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo chizikhala ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chapamphumi pakati pamaso ako; pakuti Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Aejipito adzadziwa kuti Ine ndine Yehova, polemekezedwa Ine pa Farao, pa magaleta ake, ndi pa okwera pa akavalo ake.


Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?


Ndipo Yehova ananena kwa Mose, Tsopano udzaona chomwe ndidzachitira Farao; pakuti ndi dzanja lamphamvu adzawalola apite, inde ndi dzanja lamphamvu adzawaingitsa m'dziko lake.


Chifukwa chake nena kwa ana a Israele Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aejipito ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu;


Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa padziko lonse lapansi.


M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.


Pakuti kuyambira kale anthu sanamve pena kumvetsa ndi khutu, ngakhale diso silinaone Mulungu wina popanda Inu, amene amgwirira ntchito iye amene amlindirira Iye.


Tivomereza, Yehova, chisalungamo chathu, ndi choipa cha makolo athu; pakuti takuchimwirani Inu.


Ndipo ndinalemba chikalatacho, ndichisindikiza, ndiitana mboni zambiri, ndiyesa ndalama m'miyeso.


Ife tilakwa ndi kupikisana nanu, ndipo Inu simunatikhululukire.


Koma anakaniza maweruzo anga ndi kuchita zoipa koposa amitundu, nakaniza malemba anga koposa maiko akuzungulira; pakuti anataya maweruzo anga, ndi malemba anga, sanayendemo.


tachimwa, tachita mphulupulu, tachita zoipa, tapanduka, kupatuka ndi kusiya maneno anu ndi maweruzo anu;


Ndipo mwanayo anati kwa iye, Atate ndinachimwira Kumwamba ndi pamaso panu, sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu.


Koma wamsonkhoyo alikuima patali sanafune kungakhale kukweza maso kumwamba, komatu anadziguguda pachifuwa pake nanena, Mulungu, mundichitire chifundo, ine wochimwa.


amene anatilanditsa mu imfa yaikulu yotere, nadzalanditsa; amene timyembekezera kuti adzalanditsanso;


Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa