Eksodo 13:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka m'Ejipito, m'nyumba ya akapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Tsono Mose adauza anthu kuti, “Muzikumbukira tsiku limene mudatuluka ku Ejipito, ku dziko laukapolo, chifukwa Chauta adakutulutsani kumeneko ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye chilichonse chofufumitsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Ndipo Mose anati kwa anthu, “Muzikumbukira tsiku lino, tsiku limene munatuluka mʼdziko la Igupto, dziko la ukapolo chifukwa Yehova anakutulutsani ndi dzanja lake lamphamvu. Musadye kalikonse kamene kali ndi yisiti. Onani mutuwo |
Ndipo mneneriyo, kapena wolota malotoyo, mumuphe; popeza ananena chosiyanitsa ndi Yehova Mulungu wanu, amene anakutulutsani m'dziko la Ejipito, nakuombolani m'nyumba ya ukapolo; kuti akucheteni mutaye njira imene Yehova Mulungu wanu anakulamulirani muziyendamo. Potero muzichotsa choipacho pakati pa inu.