Eksodo 13:2 - Buku Lopatulika2 Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 “Ana onse achisamba uŵapereke kwa Ine. Pakati pa Aisraele mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kaya ndi wa munthu kaya ndi wa nyama, ndi wanga ameneyo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.” Onani mutuwo |
ndi kuti tidzabwera nazo za mtanda wa mkate wathu woyamba, ndi nsembe zathu zokwera, ndi zipatso za mtengo uliwonse, vinyo, ndi mafuta, kwa ansembe, kuzipinda za nyumba ya Mulungu wathu; ndi limodzi la magawo khumi la nthaka yathu kwa Alevi; pakuti Alevi amene amalandira limodzilimodzi la magawo khumi m'midzi yonse yolima ife.