Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 13:2 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Ana onse aamuna oyamba kubadwa uwapatule, ndi anga. Aliyense woyamba kubadwa pakati pa Aisraeli ndi wanga, kaya ndi wa munthu kapena wa chiweto.”

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

2 Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Ndipatulire Ine yense woyamba kubadwa, wotsegulira pa amake mwa ana a Israele, mwa anthu ndi mwa zoweta; ndiwo anga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 “Ana onse achisamba uŵapereke kwa Ine. Pakati pa Aisraele mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kaya ndi wa munthu kaya ndi wa nyama, ndi wanga ameneyo.”

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:2
19 Mawu Ofanana  

“Tidzabweranso nawo ku Nyumba ya Mulungu, kwa ansembe amene amatumikira ku Nyumba ya Mulungu ana athu aamuna oyamba kubadwa ndi ana angʼombe oyamba kubadwa monga zalembedwera mu Malamulo. Tidzaperekanso ana oyamba kubadwa a ziweto zathu ndi ana ankhosa oyamba kubadwa.”


“Ndiponso ku zipinda za Nyumba ya Mulungu wathu, kwa ansembe tidzaperekanso mtanda wathu wa buledi wa ufa ndi mphatso zina monga zipatso za mtengo uliwonse, vinyo ndi mafuta. Tidzaperekanso kwa alevi chakhumi cha mbewu zathu pakuti alevi ndiwo amasonkhanitsa chakhumi mʼmidzi yathu yonse.


Yehova anati kwa Mose,


“Musachite chipongwe Mulungu wanu kapena kutemberera mtsogoleri wa anthu anu.


“Muzibwera ndi zipatso zoyambirira kucha zabwino kwambiri ku Nyumba ya Yehova Mulungu wanu. “Musamaphike kamwana kambuzi mu mkaka wa mayi wake.


Ndipo iwe ukati kwa Farao, ‘Yehova akuti, Israeli ali ngati mwana wanga wachisamba.’


“ ‘Ndipo unatenga ana ako aamuna ndi ana aakazi amene unandibalira ine, ndipo unakawapereka ngati nsembe kwa mafanowo. Kodi zigololo zakozo sizinakukwanire


kuti uziphanso ana anga ndi kuwapereka ngati nsembe kwa mafano akowo?


“ ‘Koma pasapezeke munthu wopereka mwana woyamba kubadwa wa nyama, popeza mwana woyamba kubadwa ali kale wa Yehova, kaya ndi ngʼombe kapena nkhosa, zimenezi ndi za Yehova.


Chilichonse choyamba kubadwa kwa munthu kaya nyama, chomwe chaperekedwa kwa Yehova ndi chako. Koma uyenera kuwombola mwana aliyense wamwamuna ndi mwana aliyense woyamba wa nyama zodetsedwa.


“Pakati pa Aisraeli onse ndatenga Alevi kulowa mʼmalo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa kwa amayi a Chiisraeli. Alevi ndi anga,


pakuti ana onse oyamba kubadwa ndi anga. Nditakantha ana onse oyamba kubadwa mu Igupto, ndinadzipatulira ndekha mwana aliyense woyamba kubadwa mu Israeli, wa munthu ndi nyama. Azikhala anga. Ine ndine Yehova.”


(Monga mmene zinalembedwera mu lamulo la Ambuye kuti, “Muzikapereka kwa Ambuye mwana aliyense wamwamuna woyamba kubadwa”),


Mumupatulire Yehova Mulungu wanu choyamba kubadwa chachimuna chilichonse pa ngʼombe ndi nkhosa zanu. Musamazigwiritse ntchito ngʼombe zoyamba kubadwa kapena kumeta nkhosa zoyamba kubadwa.


Mwafika mu mpingo wa ana oyamba kubadwa, amene mayina awo analembedwa kumwamba. Inu mwafika kwa Mulungu, woweruza anthu onse, ndiponso kwa mizimu ya anthu olungama ndi osandutsidwa kukhala angwiro.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa