Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Genesis 30:33 - Buku Lopatulika

33 Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

33 Chotero chilungamo changa chidzandivomereza m'tsogolo pamene udzandifika chifukwa cha malipiro amene ali patsogolo pako: iliyonse yosakhala yamathothomathotho ndi yamawangamawanga ya mbuzi, ndi iliyonse ya nkhosa yosakhala yakuda, ikapezedwa ndi ine, udzaiyesa yakuba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

33 Patsogolo pake mudzazindikira ngati ndachita zimenezi mokhulupirika pamene mubwere kudzaona malipiro anga. Mukadzaona kuti ndili ndi mbuzi yopanda mathotho kapena maŵanga kapena mwanawankhosa amene sali wakuda, mudzadziŵe kuti imeneyo ndi yakuba.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

33 Ndipo chilungamo changa chidzaoneka mʼtsogolo, pamene inu mudzabwere kudzaona malipiro angawo. Ngati mudzapeza mbuzi mʼgulu langa imene si yamawangamawanga, kapena mwana wankhosa wamkazi amene si wakuda ndiye kuti zimenezo zidzakhala kuti ndinakuberani.”

Onani mutuwo Koperani




Genesis 30:33
8 Mawu Ofanana  

Ndidzapita ine lero pakati pa ziweto zonse kusankhasankha m'menemo zoweta zonse zamathothomathotho ndi zamawangamawanga, ndi za nkhosa zonse, ndi mbuzi zonse zamawangamawanga ndi zamathothomathotho: zotero zidzakhala malipiro anga.


Ndipo Labani anati, Taona, kukhale monga mau ako.


Pakuti wafunafuna monse ndili nazo, kodi wapeza chiyani pa zinthu za m'nyumba mwako? Tafika nacho apa pa abale anga ndi ako, kuti aweruze pa ife tonse awiri.


Yehova anandibwezera monga mwa cholungama changa; monga mwa kuyera kwa manja anga anandipatsa mphotho.


Ndipo adzaonetsa chilungamo chako monga kuunika, ndi kuweruza kwako monga usana.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Pakuti zolakwa zathu zachuluka pamaso pa Inu, ndipo machimo athu atineneza ife; pakuti zolakwa zathu zili ndi ife, ndipo zoipa zathu tizidziwa;


Ndipo Yehova adzabwezera munthu yense chilungamo chake ndi chikhulupiriko chake, popeza Yehova anakuperekani lero m'dzanja langa, koma sindinalole kutukulira dzanja langa pa wodzozedwa wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa