Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 13:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine mu Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo ukauze mwana wako wamwamuna tsikulo, ndi kuti, Nditero chifukwa chomwe Yehova anandichitira ine potuluka ine m'Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Pa tsiku limenelo muzidzauza ana anu kuti, ‘Tikuchita zonsezi chifukwa cha zimene Chauta adatichitira pamene tinkachoka ku Ejipito.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Tsiku limenelo muzidzawuza ana anu kuti, ‘Ine ndimachita zimenezi chifukwa cha zimene Yehova anandichitira pamene ndimatuluka mʼdziko la Igupto.’

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:8
9 Mawu Ofanana  

Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.


ndi kuti ufotokozere m'makutu a ana ako, ndi a zidzukulu zako, chomwe ndidzachita mu Ejipito, ndi zizindikiro zanga zimene ndinaziika pakati pao; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.


Ndipo atate inu, musakwiyitse ana anu; komatu muwalere iwo m'maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.


Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Mbonizo, ndi malemba, ndi maweruzo, zimene Yehova Mulungu wathu anakulamulirani, zitani?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa