Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 13:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro pa dzanja lako, ndi chikumbutso pakati pa maso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa m'Ejipito ndi dzanja lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Lamulo limeneli lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa padzanja panu, kapena chikumbutso chomangidwa pamphumi panu. Motero malamulo a Chauta sadzachoka konse pakamwa panu, chifukwa Iye adakutulutsani ku Ejipito ndi dzanja lake lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Lamulo ili lidzakhala ngati chizindikiro chomangidwa pa dzanja lanu ndi chikumbutso choyikidwa pamphumi panu kuti malamulo a Yehova asachoke pakamwa panu. Pakuti Yehova anakutulutsani mʼdziko la Igupto ndi dzanja lake lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 13:9
38 Mawu Ofanana  

Ndipo awa ndi akapolo anu ndi anthu anu, amene munawaombola ndi mphamvu yanu yaikulu, ndi dzanja lanu lolimba.


Natulutsa Israele pakati pao; pakuti chifundo chake nchosatha.


Ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka; pakuti chifundo chake nchosatha.


Muli nao mkono wanu wolimba; m'dzanja mwanu muli mphamvu, dzanja lamanja lanu nlokwezeka.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Ndipo kunakhala pakutha zaka mazana anai kudza makumi atatu, inde panakhala tsiku lomwelo, makamu onse a Yehova anatuluka m'dziko la Ejipito.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo chizikhala ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chapamphumi pakati pamaso ako; pakuti Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Mose ananena ndi anthu, Kumbukirani tsiku lino limene munatuluka mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo; pakuti Yehova anakutulutsani muno ndi dzanja lamphamvu; ndipo asadye kanthu ka chotupitsa.


Ndipo ndidzatambasula dzanja langa, ndi kukantha Aejipito ndi zozizwa zanga zonse ndizichita pakati pake; ndi pambuyo pake adzakulolani kumuka.


Koma Farao sadzamvera inu, ndipo ndidzaika dzanja langa pa Aejipito, ndipo ndidzatulutsa makamu anga, anthu anga ana a Israele, m'dziko la Ejipito ndi maweruzo aakulu.


pakuti izi ndi korona wa chisomo pamutu pako, ndi mkanda pakhosi pako.


Mwananga, zisachokere kumaso ako; sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira;


mpaka muvi ukapyoza mphafa yake; amtsata monga mbalame yothamangira msampha; osadziwa kuti adzaononga moyo wake.


Undilembe pamtima pako, mokhoma chizindikiro, nundikhomenso chizindikiro pamkono pako; pakuti chikondi chilimba ngati imfa; njiru imangouma ngati manda: Kung'anima kwake ndi kung'anima kwa moto, ngati mphezi ya Yehova.


Tsiku limenelo Yehova ndi lupanga lake lolimba ndi lalikulu ndi lamphamvu adzalanga Leviyatani njoka yothamanga, ndi Leviyatani njoka yopindikapindika; nadzapha ching'ona chimene chili m'nyanja.


Taonani, Ambuye Yehova adzadza ngati wamphamvu, ndipo mkono wake udzalamulira; taonani, mphotho yake ili ndi Iye, ndipo chobwezera chake chili patsogolo pa Iye.


Wina adzati, Ine ndili wa Yehova; ndi wina adzadzitcha yekha ndi dzina la Yakobo, ndipo wina adzalemba ndi dzanja lake, Ndine wa Yehova, ndi kudzitcha yekha ndi mfunda wa Israele.


Taona ndakulembera iwe pa zikhato za manja anga; makoma ako alipo masiku onse pamaso panga.


Galamuka, galamuka, khala ndi mphamvu, mkono wa Yehova; galamuka monga masiku akale, mibadwo ya nthawi zakale. Kodi si ndiwe amene unadula Rahabu zipinjirizipinjiri; amene unapyoza chinjoka chamnyanja chija?


Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse.


Pali Ine, ati Yehova, ngakhale Koniya mwana wake wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda akadakhala mphete ya padzanja langa lamanja, ndikadachotsa iwe kumeneko;


Ndipo tsopano, Ambuye Mulungu wathu, amene munatulutsa anthu anu m'dziko la Ejipito ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri monga lero lino, tachimwa, tachita choipa.


ndipo Yehova amveketsa mau ake pamaso pa khamu lake la nkhondo; pakuti a m'chigono mwake ndi ambirimbiri; pakuti Iye wakuchita mau ake ndiye wamphamvu ndithu; pakuti tsiku la Yehova ndi lalikulu ndi loopsa ndithu; akhoza kupirira nalo ndani?


Ndipo chikhale kwa inu mphonje, yakuti muziyang'anirako, ndi kukumbukira malamulo onse a Yehova, ndi kuwachita, ndi kuti musamazondazonda kutsata za m'mtima mwanu, ndi za m'maso mwanu zimene mumatsata ndi chigololo;


Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,


Koma chitani? Mau ali pafupi ndiwe, m'kamwa mwako, ndi mumtima mwako; ndiwo mau a chikhulupiriro, amene ife tiwalalikira:


Pakuti mauwa ali pafupifupi ndi inu, m'kamwa mwanu, ndi m'mtima mwanu, kuwachita.


Ndipo uzikumbukira kuti unali kapolo m'dziko la Ejipito, ndi kuti Yehova Mulungu wako anakutulutsako ndi dzanja lamphamvu ndi mkono wotambasuka; chifukwa chake Yehova Mulungu wako anakulamulira kusunga tsiku la Sabata.


Pamenepo muzinena kwa ana anu, Tinali akapolo a Farao mu Ejipito; ndipo Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo mau awa ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu;


Ndipo muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pamaso anu.


Chifukwa chake miliri yake idzadza m'tsiku limodzi, imfa, ndi maliro, ndi njala; ndipo udzapserera ndi moto; chifukwa Ambuye Mulungu wouweruza ndiye wolimba.


nasiya Yehova Mulungu wa makolo ao, amene adawatulutsa m'dziko la Ejipito, natsata milungu ina, milungu ya mitundu ya anthu okhala pozungulira pao, naigwadira; nautsa mkwiyo wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa