Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yoswa 4:6 - Buku Lopatulika

6 kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 kuti ichi chikhale chizindikiro pakati pa inu. Akakufunsani ana anu m'tsogolomo, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani ndi inu?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Miyala imeneyi idzakhala chikumbutso, ndipo anthu azidzakumbukira zimene Chauta wachita. Ana anu akamadzakufunsani m'tsogolo muno tanthauzo lake la miyala imeneyi,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 kuti ikhale chizindikiro kwa inu. Mʼtsogolo muno ana anu akamadzakufunsani kuti, ‘Kodi miyala iyi ikutanthauza chiyani?’

Onani mutuwo Koperani




Yoswa 4:6
19 Mawu Ofanana  

Mulungu, tidamva m'makutu mwathu, makolo athu anatisimbira, za ntchitoyo mudaichita masiku ao, masiku akale.


Poteronso pokalamba ine ndi kukhala nazo imvi musandisiye, Mulungu; kufikira nditalalikira mbadwo uwu za dzanja lanu, mphamvu yanu kwa onse akudza m'mbuyo.


Ndipo tsiku lino lidzakhala kwa inu chikumbutso, muzilisunga la chikondwerero cha Yehova; ku mibadwo yanu muzilisunga la chikondwerero, likhale lemba losatha.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo chizikhala ndi iwe ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chikumbutso pakati pamaso ako; kuti chilamulo cha Yehova chikhale m'kamwa mwako; pakuti Yehova anakutulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Koma iwe, lankhula ndi ana a Israele, ndi kuti, Muzisunga masabata anga ndithu; pakuti ndiwo chizindikiro pakati pa Ine ndi inu mwa mibadwo yanu; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova wakukupatulani.


Wamoyo, wamoyo, iye adzakuyamikani inu, monga ine lero; Atate adzadziwitsa ana ake zoona zanu.


M'malo mwa mithethe mudzatuluka mtengo wamlombwa; ndi m'malo mwa lunguzi mudzamera mtengo wamchisu; ndipo chidzakhala kwa Yehova ngati mbiri, ngati chizindikiro chosatha, chimene sichidzalikhidwa.


Ndipo ndinawapatsanso masabata anga akhale chizindikiro pakati pa Ine ndi iwo, kuti adziwe kuti Ine ndine Yehova wakuwapatula.


muzipatulanso masabata anga, ndipo adzakhala chizindikiro pakati pa Ine ndi inu, kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


mbale zofukizazo za iwo amene adachimwira moyo waowao, ndipo azisule zaphanthiphanthi, zikhale chivundikiro cha guwa la nsembe; popeza anabwera nazo pamaso pa Yehova, chifukwa chake zikhala zopatulika; ndipo zidzakhala chizindikiro kwa ana a Israele.


Pakuti lonjezano lili kwa inu, ndi kwa ana anu, ndi kwa onse akutali, onse amene Ambuye Mulungu wathu adzaitana.


Ndipo muziwaphunzitsa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala inu pansi m'nyumba mwanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pakuuka inu pomwe.


koma lidzakhala mboni pakati pa ife ndi inu, ndi pakati pa mibadwo yathu ya m'tsogolo, kuti tikachita ntchito ya Yehova pamaso pake ndi nsembe zathu zopsereza, ndi zophera, ndi zoyamika; kuti ana anu asanene ndi ana athu m'tsogolomo, Mulibe gawo ndi Yehova.


Ndipo anati kwa ana a Israele, Ana anu akadzafunsa atate ao masiku akudza, ndi kuti, Miyala iyi nja chiyani?


nanena nao Yoswa, Olokani, kutsogolera likasa la Yehova Mulungu wanu pakati pa Yordani, nimudzisenzere yense mwala paphewa pake, monga mwa kuwerenga kwa mafuko a ana a Israele;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa