Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 13:17 - Buku Lopatulika

17 Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

17 Mulungu wa anthu awa Israele anasankha makolo athu, nakweza anthuwo pakugonerera iwo m'dziko la Ejipito, ndipo ndi dzanja lokwezeka anawatulutsa iwo m'menemo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

17 Mulungu wa mtundu wathu wa Aisraele, adasankha makolo athu, ndipo adaŵakuza pamene anali alendo ku dziko la Ejipito. Adaŵatulutsa m'dzikomo ndi dzanja lake lamphamvu,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

17 Mulungu wa Aisraeli anasankha makolo athu ndipo anawapatsa chuma chambiri pamene amakhala ku Igupto. Anawatulutsa mʼdzikomo ndi dzanja lake lamphamvu.

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 13:17
42 Mawu Ofanana  

Pakuti Yehova anadzisankhira Yakobo, Israele, akhale chuma chake chenicheni.


Ndipo kunakhala tsiku lomwelo, kuti Yehova anatulutsa ana a Israele m'dziko la Ejipito, monga mwa makamu ao.


Ndipo kudzakhala, akakufunsa mwana wako masiku akudzawo ndi kuti, Ichi nchiyani? Ukanene naye, Yehova anatitulutsa mu Ejipito, m'nyumba ya ukapolo, ndi dzanja lamphamvu;


Ndipo chizikhala ngati chizindikiro padzanja lako, ndi chapamphumi pakati pamaso ako; pakuti Yehova anatitulutsa mu Ejipito ndi dzanja lamphamvu.


Ndipo Yehova analimbitsa mtima wa Farao, mfumu ya Aejipito, ndipo iye analondola ana a Israele; koma ana a Israele adatuluka ndi dzanja lokwezeka.


Tsopano ndidziwa kuti Yehova ali wamkulu ndi milungu yonse, pakuti momwe anadzikuza okha momwemo anawaposa.


Koma tsopano, imva Yakobo, mtumiki wanga, ndi Israele, amene ndakusankha;


Ndipo ndinakukwezani kuchokera m'dziko la Ejipito, ndi kukutsogolerani zaka makumi anai m'chipululu, kuti mulandire dziko la Aamori likhale cholowa chanu.


Pakuti ndinakukwezani kukutulutsani m'dziko la Ejipito, ndi kuombola inu m'nyumba ya ukapolo; ndipo ndinatuma akutsogolereni Mose, Aroni, ndi Miriyamu.


Makolo anu anatsikira ku Ejipito ndiwo anthu makumi asanu ndi awiri; ndipo Yehova Mulungu wanu anakusandulizani tsopano muchuluke ngati nyenyezi za kumwamba.


Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa Iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope padziko lapansi.


Koma Yehova anakutengani, nakutulutsani m'ng'anjo yamoto, mu Ejipito, mukhale kwa Iye anthu a cholowa chake, monga mukhala lero lino.


Kapena kodi anayesa Mulungu kumuka ndi kudzitengera mtundu mwa mtundu wina wa anthu, ndi mayesero, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi nkhondo, ndi mwa dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, ndi mwa zoopsa zazikulu, monga mwa zonse Yehova Mulungu wanu anakuchitirani mu Ejipito pamaso panu?


Ndipo popeza anakonda makolo anu, anasankha mbeu zao zakuwatsata, nakutulutsani pamaso pake ndi mphamvu yake yaikulu, mu Ejipito;


mayesero aakulu maso anu anawapenya, ndi zizindikiro, ndi zozizwa, ndi dzanja lamphamvu, ndi mkono wotambasuka, zimene Yehova Mulungu wanu anakutulutsani nazo; Yehova Mulungu wanu adzatero nayo mitundu yonse ya anthu imene muwaopa.


Simulowa kulandira dziko lao chifukwa cha chilungamo chanu, kapena mtima wanu woongoka; koma Yehova Mulungu wanu awapirikitsa pamaso panu chifukwa cha zoipa za amitundu awa, ndi kuti akhazikitse mau amene Yehova analumbirira makolo anu, Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Tsoka kwa ife! Adzatilanditsa ndani m'manja a milungu yamphamvu imeneyi? Milungu ija inakantha Aejipito ndi masautso onse m'chipululu ndi yomweyi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa