Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


113 Mau a m'Baibulo Okhudza Ndalama

113 Mau a m'Baibulo Okhudza Ndalama

Nthaŵi zambiri timaganiza kuti kukhala ndi ndalama zokwanira kumatanthauza chuma chambiri ndi katundu wambiri. Koma, m’mawu a Mulungu sitikuuzidwa zimenezo. Ngakhale timaŵerenga nkhani za anthu opembedza komanso olemera, monga Abrahamu ndi Solomo, komanso oipa monga Nabala (1 Samueli 25:2-36), ngakhale Khristu sanakhale mochuluka, koma zosowa zake zonse zimakwaniritsidwa nthawi zonse.

Malemba amatiuza kuti: “Pakuti sitinabwere ndi kanthu m’dziko lino lapansi, ndipo sitingatulerenso kanthu. Chifukwa chake, pokhala ndi chakudya ndi zovala, tikhale okhutira nazo. Pakuti iwo amene afuna kukhala achuma amagwera m’chiyeso, ndi m’msampha, ndi m’zilakolako zambiri zopusa ndi zopweteka, zimene zimiza anthu m’chiwonongeko ndi m’chitayiko; pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha ndalama, chimene ena pochilakalaka anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zisoni zambiri.” (1 Timoteo 6:7-10).

Monga momwe tiyenera kulemekeza Mulungu m’mbali zina za moyo wathu, kumvera Mulungu pankhani ya zachuma kudzabweretsa madalitso ndi mtendere, ndipo kudzatithandiza kukhala bwino ndi ena.




1 Timoteyo 5:8

Koma ngati wina sadzisungiratu mbumba yake ya iye yekha, makamaka iwo a m'banja lake, wakana chikhulupiriro iye, ndipo aipa koposa wosakhulupirira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:38

Patsani, ndipo kudzapatsidwa kwa inu; muyeso wabwino, wotsendereka, wokuchumuka, wosefukira, anthu adzakupatsani m'manja mwanu. Pakuti kudzayesedwa kwa inu ndi muyeso womwewo muyesa nao inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:22

Madalitso a Yehova alemeretsa, saonjezerapo chisoni.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:8

Musakhale ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko; pakuti iye amene akondana ndi mnzake wakwanitsa lamulo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:35

M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:21

pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:8

Ndipo Mulungu akhoza kuchulukitsira chisomo chonse kwa inu; kuti inu, pokhala nacho chikwaniro chonse m'zinthu zonse, nthawi zonse, mukachulukire kuntchito yonse yabwino;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21

Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17

Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 13:2

Ndipo Abramu anali wolemera ndithu ndi ng'ombe ndi siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:25

Ukakongoletsa ndalama anthu anga osauka okhala nanu, usamkhalira ngati wangongole; usamuwerengera phindu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:10

Mubwere nalo limodzilimodzi lonse la khumi, kunyumba yosungiramo, kuti m'nyumba mwanga mukhale chakudya; ndipo mundiyese nako tsono, ati Yehova wa makamu, ngati sindikutsegulirani mazenera a kumwamba, ndi kukutsanulirani mdalitso wakuti adzasoweka malo akuulandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:9

Mwini diso lamataya adzadala; pakuti apatsa osauka zakudya zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:10

Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 3:9

Lemekeza Yehova ndi chuma chako, ndi zinthu zako zonse zoyambirira kucha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:11

Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 41:34-36

Farao achite chotere, alembe woyang'anira dziko wosonkhetsa limodzi la magawo asanu la dziko la Ejipito m'zaka zisanu ndi ziwiri zakuchuluka dzinthu. Iwo asonkhanitse chakudya chonse cha zaka zabwino izo zilinkudzazo, aunjike tirigu m'manja a Farao akhale chakudya m'mizinda, namsunge. Ndipo chakudyacho chidzakhala m'dziko chosonkhera zaka zisanu ndi ziwiri za njala imene idzakhala m'dziko la Ejipito; kuti dziko lisaonongedwe ndi njala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28

Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:18

kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:11

Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 28:4

mwa nzeru zako ndi luntha lako wadzionerera chuma, wadzionereranso golide ndi siliva mwa chuma chako;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:20

Mokhala wanzeru muli katundu wofunika ndi mafuta; koma wopusa angozimeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:13

Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:8-9

Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:22

Wabwino asiyira zidzukulu zake cholowa chabwino; koma wochimwa angosungira wolungama chuma chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 3:8-9

Kodi munthu adzalanda za Mulungu? Ndipo inu mundilanda Ine. Koma mukuti, Takulandani zotani? Limodzilimodzi la magawo khumi, ndi zopereka. Mutembereredwa ndi temberero; pakuti mundilanda Ine, ndinu mtundu uwu wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 21:1-4

Ndipo Yesu anakweza maso, naona anthu eni chuma alikuika zopereka zao mosungiramo ndalama. Pamenepo ananena nao, Mtundu wa anthu udzaukira pa mtundu wina, ndipo ufumu pa ufumu wina: ndipo kudzakhala zivomezi zazikulu, ndi njala ndi miliri m'malo akutiakuti, ndipo kudzakhala zoopsa ndi zizindikiro zazikulu zakumwamba. Koma zisanachitike izi, anthu adzakuthirani manja, nadzakuzunzani, nadzapereka inu ku masunagoge ndi ndende, nadzamuka nanu kwa mafumu ndi akazembe, chifukwa cha dzina langa. Kudzakhala kwa inu ngati umboni. Chifukwa chake tsimikizani mumtima mwanu, kuti usanafike mlandu musalingirire chimene mudzayankha. Pakuti Ine ndidzakupatsani inu kamwa ndi nzeru, zimene adani anu onse sadzatha kuzikana kapena kuzitsutsa. Koma mudzaperekedwa ngakhale ndi akukubalani, ndi abale, ndi a fuko lanu, ndi abwenzi anu; ndipo ena a inu adzakuphani. Ndipo anthu onse adzadana ndi inu chifukwa cha dzina langa. Ndipo silidzaonongeka tsitsi limodzi la pamutu panu. Mudzakhala nao moyo wanu m'chipiriro. Ndipo anaona mkazi wina wamasiye waumphawi alikuika momwemo timakobiri tiwiri. Koma pamene paliponse mudzaona Yerusalemu atazingidwa ndi magulu a ankhondo, zindikirani pamenepo kuti chipulumutso chake chayandikira. Pamenepo iwo ali mu Yudeya athawire kumapiri, ndi iwo ali m'kati mwa uwo atuluke, ndi iwo ali kuminda asalowemo. Chifukwa amenewa ndi masiku akubwezera, kuti zonse zidalembedwa zichitike. Koma tsoka iwo akukhala ndi pakati, ndi iwo akuyamwitsa ana masiku awo! Pakuti padzakhala chisauko chachikulu padziko, ndi mkwiyo pa anthu awa. Ndipo adzagwa ndi lupanga lakuthwa, nadzagwidwa ndende kunka kumitundu yonse ya anthu; ndipo mapazi a anthu akunja adzapondereza Yerusalemu kufikira kuti nthawi zao za anthu akunja zakwanira. Ndipo kudzakhala zizindikiro pa dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi; ndi padziko lapansi chisauko cha mitundu ya anthu, alikuthedwa nzeru pa mkokomo wake wa nyanja ndi mafunde ake; anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi; pakuti mphamvu zakumwamba zidzagwedezeka. Ndipo pamenepo adzaona Mwana wa Munthu alinkudza mu mtambo ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu. Koma poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira. Ndipo ananena nao fanizo; Onani mkuyu, ndi mitengo yonse: Ndipo Iye anati, Zoonadi ndinena kwa inu, wamasiye uyu waumphawi anaikamo koposa onse; pamene iphukira, muipenya nimuzindikira pa nokha kuti dzinja lili pafupi pomwepo. Inde chotero inunso, pakuona zinthu izi zilikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi. Indetu ndinena ndinu, Mbadwo uno sudzapitirira, kufikira zonse zitachitika. Thambo ndi dziko lapansi zidzapita; koma mau anga sadzapita. Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope padziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika, ndi kuimirira pamaso pa Mwana wa Munthu. Ndipo usana uliwonse Iye analikuphunzitsa mu Kachisi; ndi usiku uliwonse anatuluka, nagona paphiri lotchedwa la Azitona. Ndipo anthu onse analawira mamawa kudza kwa Iye ku Kachisi kudzamvera Iye. pakuti onse amenewa anaika mwa unyinji wao pa zoperekazo; koma iye mwa kusowa kwake anaikamo za moyo wake, zonse anali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:7-8

Wodala munthu amene akhulupirira Yehova, amene chikhulupiriro chake ndi Yehova. Ndipo adzakhala ngati mtengo wooka kuli madzi, wotambalitsa mizu yake pamtsinje, wosaopa pofika nyengo yadzuwa, koma tsamba lake likhala laliwisi; ndipo suvutika chaka cha chilala, suleka kubala zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:1

Muyeso wonyenga unyansa Yehova; koma mulingo wamphumphu umsekeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 25:35-37

Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu. Usamambwezetsa phindu, kapena chionjezero; koma uope Mulungu wako; kuti mbale wako akhale nawe. Musamampatsa ndalama zako polira phindu, kapena kumpatsa zakudya kuti aonjezerepo pochibwezera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 8:18

Koma mukumbukire Yehova Mulungu wanu, popeza ndi Iyeyu wakupatsani mphamvu yakuonera chuma; kuti akhazikitse chipangano chake chimene analumbirira makolo anu, monga chikhala lero lino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:7-8

Akakhala ndi inu munthu waumphawi, ndiye wina wa abale anu, mu umodzi wa midzi yanu, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musakhakala mtima wanu, kapena kuumitsa dzanja lanu kukaniza mbale wanu waumphawi; koma muzimtansira dzanja lanu ndithu ndi kumkongoletsa ndithu zofikira kusowa kwake, monga umo amasowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 23:19-20

Musamakongoletsa mbale wanu mopindulitsa; phindu la ndalama, phindu la chakudya, phindu la kanthu kalikonse kokongoletsa. Mwana wa m'chigololo asalowe m'msonkhano wa Yehova, ngakhale mbadwo wake wakhumi usalowe m'msonkhano wa Yehova. Mukongoletse mlendo mopindulitsa; koma mbale wanu musamamkongoletsa mopindulitsa, kuti Yehova Mulungu wanu akudalitseni mwa zonse muzigwira ndi dzanja lanu, m'dziko limene mulowamo kulilandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12

Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:47-48

Popeza simunatumikire Yehova Mulungu wanu ndi chimwemwe ndi mokondwera mtima, chifukwa cha kuchuluka zinthu zonse; chifukwa chake mudzatumikira adani anu amene Yehova adzakutumizirani, ndi njala, ndi ludzu, ndi usiwa, ndi kusowa zinthu zonse; ndipo adzaika goli lachitsulo pakhosi panu, kufikira atakuonongani.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 28:12-13

Yehova adzakutsegulirani chuma chake chokoma, ndicho thambo la kumwamba, kupatsa dziko lanu mvula m'nyengo yake, ndi kudalitsa ntchito zonse za dzanja lanu; ndipo mudzakongoletsa amitundu ambiri, osakongola nokha. Ndipo Yehova adzakuyesani mutu, si mchira ai; ndipo mudzakhala wa pamwamba pokha, si wapansi ai; ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, amene ndikuuzani lero, kuwasunga ndi kuwachita;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 10:23

Ndipo mfumu Solomoni anawaposa mafumu onse a dziko lapansi pa chuma ndi nzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:12

Zolemera ndi ulemu zifuma kwanu, ndipo muchita ufumu pa zonse, ndi m'dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m'dzanja lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mbiri 29:16

Yehova Mulungu wathu, zounjikika izi zonse tazikonzeratu kukumangirani Inu nyumba ya dzina lanu loyera zifuma ku dzanja lanu, zonsezi ndi zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 1:11-12

Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao, nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 31:5-6

Ndipo pobuka mau aja, ana a Israele anapereka mochuluka, zobala zoyamba za tirigu, vinyo, ndi mafuta, ndi uchi, ndi za zipatso zonse za m'minda, ndi limodzi la magawo khumi la zonse anabwera nazo mochuluka. Ndi ana a Israele ndi Yuda okhala m'mizinda ya Yuda, iwonso anabwera nalo limodzi la magawo khumi la ng'ombe, ndi nkhosa, ndi limodzi la magawo khumi la zinthu zopatulika, zopatulikira Yehova Mulungu wao; naziunjika miyulumiyulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 32:27-29

Ndipo chuma ndi ulemu zinachulukira Hezekiya, nadzimangira iye zosungiramo siliva, ndi golide, ndi timiyala ta mtengo wake, ndi zonunkhira, ndi zikopa, ndi zipangizo zokoma zilizonse; ndi nyumba zosungiramo zipatso za tirigu, ndi vinyo, ndi mafuta, ndi zipinda za nyama iliyonse, ndi makola a zoweta. Nadzimangiranso mizinda, nadzionera nkhosa ndi ng'ombe zochuluka; pakuti Mulungu adampatsa chuma chambirimbiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Nehemiya 5:11

Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:6-8

Pita kunyerere, waulesi iwe, penya njira zao nuchenjere; zilibe mfumu, ngakhale kapitao, ngakhale mkulu; koma zitengeratu zakudya zao m'malimwe; ndipo zituta dzinthu zao m'masika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:4

Wochita ndi dzanja laulesi amasauka; koma dzanja la akhama lilemeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:4

Chuma sichithandiza tsiku la mkwiyo; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24-25

Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka. Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:23

M'ntchito zonse muli phindu; koma kulankhulalankhula kungopatsa umphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16

Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:27

Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:3

Pereka zochita zako kwa Yehova, ndipo zolingalira zako zidzakhazikika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Zapang'ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 17:18

Munthu wosowa nzeru apangana kulipirira wina, napereka chikole pamaso pa mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:17

Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova; adzambwezera chokoma chakecho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:5

Zoganizira za wakhama zichulukitsadi katundu; koma yense wansontho angopeza umphawi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:1

Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:16

Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:26-27

Usakhale wodulirana mpherere, ngakhale kumperekera chikole cha ngongole zake. Ngati ulibe chobwezera kodi achotserenji kama lako pansi pako?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4-5

Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:27

Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 27:23-24

Udziwitsitse zoweta zako zili bwanji, samalira magulu ako; pakuti chuma sichili chosatha; kodi korona alipobe mpaka mibadwomibadwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:19

Inde yemwe Mulungu wamlemeretsa nampatsa chuma, namninkhanso mphamvu ya kudyapo, ndi kulandira gawo lake ndi kukondwera ndi ntchito zake; umenewu ndiwo mtulo wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 7:12

Pakuti nzeru itchinjiriza monga ndalama zitchinjiriza; koma kudziwa kupambana, chifukwa nzeru isunga moyo wa eni ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:2

Bwanji inu mulikutayira ndalama chinthu chosadya, ndi kutayira malipiro anu zosakhutitsa? Mverani Ine mosamalitsa, nimudye chimene chili chabwino, moyo wanu nukondwere ndi zonona.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:11

Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hagai 2:8

Siliva ndi wanga, golide ndi wanga, ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 16:26

Pakuti munthu adzapindulanji, akalandira dziko lonse, nataya moyo wake? Kapena munthu adzaperekanji chosintha ndi moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta; Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 4:19

ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33-34

Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28-30

Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:10-12

Iye amene akhulupirika m'chaching'onong'ono alinso wokhulupirika m'chachikulu; ndipo iye amene ali wosalungama m'chachikulu. Chifukwa chake ngati simunakhale okhulupirika m'chuma cha chosalungama, adzakhulupirira inu ndani ndi chuma choona? Ndipo ngati simunakhale okhulupirika ndi zake za wina, adzakupatsani inu ndani za inu eni?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:13

Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 19:11-27

Ndipo pakumva izi iwo, Iye anaonjeza nanena fanizo, chifukwa anali Iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti Ufumu wa Mulungu ukuti uonekere pomwepo. Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka kudziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi za mina, nati kwaiwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. Koma mfulu za pamudzi pake zinamuda, nkutuma akazembe amtsate m'mbuyo ndi kunena, Ife sitifuna munthuyo akhale mfumu yathu. Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziwe umo anapindulira pochita malonda. Ndipo anafika woyamba, nanena, Mbuye, mina yanu inachita nionjeza mina khumi. Ndipo anati kwa iye, Chabwino, kapolo wabwino iwe; popeza unakhala wokhulupirika m'chaching'onong'ono, khala nao ulamuliro pa mizinda khumi. Ndipo anadza wachiwiri, nanena, Mbuye, mina yanu yapindula mina zisanu. Ndipo anati kwa iyenso, Khala iwenso woweruza mizinda isanu. Ndipo taonani, mwamuna wotchedwa dzina lake Zakeyo; ndipo iye anali mkulu wa amisonkho, nali wachuma. Ndipo wina anadza, nanena, Mbuye, taonani, siyi mina yanu, ndaisunga m'kansalu; pakuti ndinakuopani, popeza inu ndinu munthu wouma mtima: munyamula chimene simunachiike pansi, mututa chimene simunachifese. Ananena kwa iye, Pakamwa pako ndikuweruza, kapolo woipa iwe. Unadziwa kuti ine ndine munthu wouma mtima, wonyamula chimene sindinachiike, ndi wotuta chimene sindinachifese; ndipo sunapereke bwanji ndalama yanga pokongoletsa, ndipo ine pakudza ndikadaitenga ndi phindu lake? Ndipo anati kwa iwo akuimirirapo, Mchotsereni minayo, nimuipatse kwa iye wakukhala nazo mina khumi. Ndipo anati kwa iye, Mbuye, ali nazo mina khumi. Ndinena ndi inu, kuti kwa yense wakukhala nacho kudzapatsidwa; koma kwa iye amene alibe kanthu, chingakhale chimene ali nacho chidzachotsedwa. Koma adani anga aja osafuna kuti ndidzakhala mfumu yao, bwerani nao kuno, nimuwaphe pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 2:44-45

Ndipo onse akukhulupirira anali pamodzi, nakhala nazo zonse zodyerana. Ndipo zimene anali nazo, ndi chuma chao, anazigulitsa, nazigawira kwa onse, monga momwe yense anasowera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 4:34-35

Pakuti mwa iwo munalibe wosowa; pakuti onse amene anali nayo minda, kapena nyumba, anazigulitsa nabwera nao malonda ake a izo adazigulitsa, nawaika pa mapazi a atumwi; ndipo anagawira yense monga kusowa kwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:13

Patsani zosowa oyera mtima; cherezani aulendo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 4:2

Komatu pano pafunika za adindo, kuti munthu akhale wokhulupirika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 16:2

Tsiku loyamba la sabata yense wa inu asunge yekha, monga momwe anapindula, kuti zopereka zisachitike pakudza ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:2

kuti m'chitsimikizo chachikulu cha chisautso, kuchulukitsa kwa chimwemwe chao, ndi kusauka kwao, kwenikweni zidachulukira ku cholemera cha kuolowa mtima kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:9

Pakuti mudziwa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:6-7

Koma nditi ichi, kuti iye wakufesa mouma manja, mouma manjanso adzatuta. Ndipo iye wakufesa moolowa manja, moolowa manjanso adzatuta. Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:10-11

Ndipo iye wopatsa mbeu kwa wofesa, ndi mkate ukhale chakudya, adzapatsa ndi kuchulukitsa mbeu yanu yofesa, nadzaonjezapo pa zipatso za chilungamo chanu; polemeretsedwa inu m'zonse kukuolowa manja konse, kumene kuchita mwa ife chiyamiko cha kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:11-13

Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:23-24

chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima, monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ai; podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 4:11-12

ndi kuti muyesetse kukhala chete ndi kuchita za inu eni ndi kugwira ntchito ndi manja anu, monga tinakuuzani; kuti mukayende oona mtima pa iwo a kunja, ndi kukhala osasowa kanthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:17-19

Lamulira iwo achuma m'nthawi ino ya pansi pano, kuti asadzikuze, kapena asayembekezere chuma chosadziwika kukhala kwake, koma Mulungu, amene atipatsa ife zonse kochulukira, kuti tikondwere nazo; kuti achite zabwino, nachuluke ndi ntchito zabwino, nakondwere kugawira ena, nayanjane; nadzikundikire okha maziko okoma ku nyengo ikudzayi, kuti akagwire moyo weniweniwo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:14

Ndipo anthu athu aphunzirenso asunge ntchito zabwino zofunika, kuti asakhale osabala zipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:5

Koma wina wa inu ikamsowa nzeru, apemphe kwa Mulungu, amene apatsa kwa onse modzala manja, niwosatonza; ndipo adzampatsa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:15-16

Mbale kapena mlongo akakhala wausiwa, ndi kusowa chakudya cha tsiku lake, ndipo wina wa inu akanena nao, Mukani ndi mtendere, mukafunde ndi kukhuta; osawapatsa iwo zosowa za pathupi; kupindula kwake nchiyani?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:13-15

Nanga tsono, inu akunena, Lero kapena mawa tidzapita kulowa kumudzi wakutiwakuti, ndipo tidzagonerako ndi kutsatsa malonda, ndi kupindula nao; inu amene simudziwa chimene chidzagwa mawa. Moyo wanu uli wotani? Pakuti muli utsi, wakuonekera kanthawi, ndi pamenepo ukanganuka. Mukadanena inu, Akalola Ambuye, ndipo tikakhala ndi moyo, tidzachita kakutikakuti.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:1-3

Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:4

Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:10

monga yense walandira mphatso, mutumikirane nayo, ngati adindo okoma a chisomo cha mitundumitundu cha Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2-3

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu; osati monga ochita ufumu pa iwo a udindo wanu, koma okhala zitsanzo za gululo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
3 Yohane 1:2

Wokondedwa, ndipemphera kuti pa zonse ulemere, nukhale bwino, monga mzimu wako ulemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 3:17-18

Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa; ndikulangiza ugule kwa Ine golide woyengeka m'moto, kuti ukakhale wachuma, ndi zovala zoyera, kuti ukadziveke, ndi kuti manyazi a usiwa wako asaoneke; ndi mankhwala opaka m'maso mwako, kuti ukaone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 15:10

Muzimpatsa ndithu, osawawa mtima wanu pompatsa; popeza, chifukwa cha ichi Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani mu ntchito zanu zonse, ndi m'zonse muikapo dzanja lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:28

Wokhulupirira chuma chake adzagwa; koma olungama adzaphuka ngati tsamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 18:11

Chuma cha wolemera ndicho mzinda wake wolimba; alingalira kuti ndicho khoma lalitali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 11:1-2

Ponya zakudya zako pamadzi; udzazipeza popita masiku ambiri. Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe. Gawira asanu ndi awiri ngakhale asanu ndi atatu; pakuti sudziwa choipa chanji chidzaoneka pansi pano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 8:3

ndi Yohana, mkazi wake wa Kuza kapitao wa Herode, ndi Suzana, ndi ena ambiri, amene anawatumikira ndi chuma chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye, ndikudza kwa Inu, podziwa kuti Inu nokha ndinu kasupe wa chilichonse, ndi Inu amene mupati mphamvu zopezera chuma. Ndikupemphani kuti mundipatse nzeru zoyendetsera bwino ndalama zanga, osati kuzidalira, koma kubweretsa kusintha kwathunthu m'moyo wanga ndi m'banja langa malinga ndi mawu anu. Mundithandize kuzindikira nthawi zonse kuti Inu ndinu wopereka zinthu zonse, ndipo tsiku lililonse mumandalitsa kuti ndithandize ena. Mundithandize kukhala mwana wanu wochita chakhumi mokhulupirika, kuteteza mtima wanga ku umbombo ndi kusirira. Mundithandize kukhala paubwenzi wolimba ndi Inu, kuti ndizindikire kuti palibe changa, koma zonse zimachokera m'manja mwanu. Ndikufuna kumamatira kwambiri ku mawu anu, chifukwa ndiwo chitsimikizo changa chokhala woyang'anira bwino ndalama zanga, kuti ndipambane m'mbali zonse za moyo wanga. Zikomo chifukwa munadzichepetsa kuti ine ndilemere, kundiombola ku umphawi, kuvutika, ndi kusowa. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa