Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 14:28 - Buku Lopatulika

28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

28 Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

28 “Wina mwa inu akafuna kumanga nyumba yosanja, kodi suja amayamba wakhala pansi nkuŵerenga ndalama zofunika, kuti aone ngati ali nazo zokwanira kuitsiriza?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

28 “Taganizani, ngati wina mwa inu akufuna kumanga nsanja, kodi iye sayamba wakhala pansi ndi kuganizira za mtengo wake kuti aone ngati ali ndi ndalama zokwanira kuti atsirizire?

Onani mutuwo Koperani




Luka 14:28
12 Mawu Ofanana  

Longosola ntchito yako panjapo, nuikonzeretu kumunda; pambuyo pake ndi kumanga nyumba yako.


Ndipo adzada inu anthu onse chifukwa cha dzina langa; koma iye wakupirira kufikira chimaliziro, iyeyu adzapulumutsidwa.


Ndipo Yesu ananena kwa iye, Ankhandwe ali nazo nkhwimba zao, ndi mbalame za m'mlengalenga zisa zao, koma Mwana wa Munthu alibe potsamira mutu wake.


Ndipo aliyense amene sasenza mtanda wake wa mwini yekha, ndi kudza pambuyo panga, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye,


Chifukwa chake tsono, yense wa inu amene sakaniza zonse ali nazo, sangathe kukhala wophunzira wanga.


Pamenepo Paulo anayankha, Muchitanji, polira ndi kundiswera mtima? Pakuti ndakonzeka ine si kumangidwa kokha, komatunso kufera ku Yerusalemu chifukwa cha dzina la Ambuye Yesu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa