Nehemiya 5:11 - Buku Lopatulika11 Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Muŵabwezere lero lomwe lino minda yao, mitengo yao yamphesa, mitengo yao ya olivi, ndi nyumba zao, ndipo muŵakhululukire ngongole za ndalama, za tirigu, za vinyo, ndi za mafuta, zimene mudaaŵakongoza.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Abwezereni lero lomwe minda yawo, mitengo ya mphesa, mitengo ya olivi ndiponso nyumba zawo. Muwabwezerenso chiwongoladzanja cha ndalama, tirigu, vinyo ndi mafuta zimene munatenga.” Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.