Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 5:12 - Buku Lopatulika

12 Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Pamenepo anati, Tidzawabwezera osawalipitsa kanthu, tidzachita monga momwe mwanena. Pamenepo ndinaitana ansembe, ndi kuwalumbiritsa, kuti adzachita monga mwa mau awa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Ndiye iwowo adayankha kuti, “Tidzachitadi monga mukuneneramu. Tidzabwezera zimenezi osapemphapo kanthu.” Pamenepo ndidaitana ansembe, ndipo pamaso pao ndidaŵalumbiritsa akuluwo kuti adzachitedi monga momwe adalonjezera.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Iwo anayankha kuti, “Ife tidzawabwezera zimenezi popanda kupemphapo kanthu kalikonse kwa iwo. Tidzachita monga mwanena.” Pambuyo pake ndinayitanitsa ansembe ndipo pamaso pawo ndinawalumbiritsa atsogoleriwo ndi akuluakuluwo kuti adzachitadi zomwe analonjezazo.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 5:12
15 Mawu Ofanana  

Ndipo unayankha msonkhano wonse, ndi kunena ndi mau aakulu, Monga mwa mau anu tiyenera kuchita.


Nanyamuka Ezara, nalumbiritsa akulu a ansembe, ndi Alevi, ndi Aisraele onse, kuti adzachita monga mwa mau awa. Nalumbira iwo.


amenewa anaumirira abale ao, omveka ao, nalowa m'temberero ndi lumbiro, kuti adzayenda m'chilamulo cha Mulungu anachipereka Mose mtumiki wa Mulungu, ndi kuti adzasunga ndi kuchita zonse atilamulira Yehova Ambuye wathu, ndi maweruzo ake, ndi malemba ake;


ndi kuti sitidzapereka ana athu aakazi kwa mitundu ya anthu a m'dziko, kapena kutengera ana athu aamuna ana ao aakazi;


ndipo mitundu ya anthu a m'dziko akabwera nao malonda, ngakhale tirigu, tsiku la Sabata, kutsata malonda, sitidzagulana nao pa tsiku la Sabata, kapena tsiku lina lopatulika, ndi kuti tidzaleka chaka chachisanu ndi chiwiri ndi mangawa ali onse.


Ndipo ndinatsutsana nao, ndi kuwatemberera, ndi kukantha ena a iwo, ndi kumwetula tsitsi lao, ndi kuwalumbiritsa pa Mulungu ndi kuti, Musapereke ana anu aakazi kwa ana ao aamuna, kapena kutengera ana anu aamuna, kapena a inu nokha, ana ao aakazi.


Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.


Koma Yesu anangokhala chete. Ndipo mkulu wa ansembe ananena kwa Iye, Ndikulumbiritsa Iwe pa Mulungu wamoyo, kuti utiuze ife ngati Iwe ndiwe Khristu, Mwana wa Mulungu.


Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa