Nehemiya 5:13 - Buku Lopatulika13 Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201413 Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa13 Tsono ndidakutumula chovala changa ndipo ndidanena kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu aliyense wosasunga malonjezo akeŵa. Amsandutse mmphaŵi pakumlanda nyumba yake, antchito ake ndi zonse zimene ali nazo.” Apo msonkhano wonse udavomereza ponena kuti, “Zikhale momwemo ndithu!” Ndipo onsewo adatamanda Chauta. Pambuyo pake akulu aja adachita monga m'mene adaalonjezera. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero13 Ndipo inenso ndinakutumula chovala changa ndi kuti, “Chimodzimodzinso Mulungu akutumule munthu wosasunga malonjezano ake. Amulande nyumba yake ndi katundu wake ndi kumusandutsa mʼmphawi!” Apo msonkhano wonse unati, “Ameni” natamanda Yehova. Ndipo anthu aja anachita monga analonjezera. Onani mutuwo |