Nehemiya 5:14 - Buku Lopatulika14 Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadye chakudya cha kazembe. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201414 Ndipo chiyambire tsiku lija anandiika ndikhale kazembe wao m'dziko la Yuda; kuyambira chaka cha makumi awiri kufikira chaka cha makumi atatu mphambu ziwiri cha Arita-kisereksesi mfumu, ndizo zaka khumi ndi ziwiri, ine ndi abale anga sitinadya chakudya cha kazembe. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa14 Kuyambiranso nthaŵi imene adandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa m'dziko la Yuda, kuchokera chaka cha 20 mpaka chaka cha 32 cha ufumu wa Arita-kisereksesi, ndiye kuti zaka khumi ndi ziŵiri, ineyo ndi abale anga sitidalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero14 Ndiponso kuyambira nthawi imene anandisankha kuti ndikhale bwanamkubwa wa dziko la Yuda, kuchokera chaka cha makumi awiri mpaka chaka cha 32 muulamuliro wa ufumu wa Aritasasita, ndiye kuti kwa zaka zokwana 12, ine ngakhale abale anga sitinalandire chakudya choyenerera bwanamkubwa. Onani mutuwo |