Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Nehemiya 5:15 - Buku Lopatulika

15 Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 Koma akazembe akale ndisanakhale ine, analemetsa anthu, nadzitengera kwa iwo mkate, ndi vinyo, pamodzi ndi siliva masekeli makumi anai; angakhale anyamata ao anachita ufumu pa anthu; koma sindinatero ine, chifukwa cha kuopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Abwanamkubwa amene analipo kale ankasautsa anthu pomaŵalanda chakudya ndi vinyo, ndi kuŵalipitsanso masekeli asiliva makumi anai. Ngakhale antchito ao nawonso ankathinitsa anthu. Koma ine sindidachite nawo zimenezo, popeza kuti ndinkaopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Koma abwanamkubwa akale ankasautsa anthu. Iwo ankalanda anthu chakudya ndi vinyo ndi kuwalipiritsanso masekeli asiliva makumi anayi. Ngakhalenso antchito awo amavutitsa anthu kwambiri. Koma ine sindinachite zimenezo chifukwa ndimaopa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Nehemiya 5:15
19 Mawu Ofanana  

Ndipo Abrahamu anati, Chifukwa ndinati, Pompano palibe ndithu kumuopa Mulungu, ndipo adzandipha ine chifukwa cha mkazi wanga.


Ndipo Yosefe anati kwa iwo tsiku lachitatu, Chitani ichi, kuti mukhale ndi moyo; ine ndiopa Mulungu;


Ndiponso ndinalimbikira ntchito ya linga ili, ngakhale dziko sitinaligule, ndi anyamata anga onse anasonkhanira ntchito komweko.


Ndinatinso, Chinthu muchitachi si chokoma ai; simuyenera kodi kuyenda m'kuopa Mulungu wathu, chifukwa cha mnyozo wa amitundu, ndiwo adani athu?


Pakuti tsoka lochokera kwa Mulungu linandiopsa, ndi chifukwa cha ukulu wake sindinakhoza kanthu.


Aleluya. Wodala munthu wakuopa Yehova, wakukondwera kwambiri ndi malamulo ake.


Yehova akondwera nao akumuopa Iye, iwo akuyembekeza chifundo chake.


Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.


Mkulu akamvera chinyengo, atumiki ake onse ali oipa.


Ndani ali mwa inu amene amaopa Yehova, amene amamvera mau a mtumiki wake? Iye amene ayenda mumdima, ndipo alibe kuunika, akhulupirire dzina la Yehova, ndi kutsamira Mulungu wake.


Ndipo ndinagula mundawo wa ku Anatoti kwa Hanamele mwana wa mbale wa atate wanga, ndimyesera ndalama, masekeli khumi ndi asanu ndi awiri a siliva.


Akapolo atilamulira; palibe wotipulumutsa m'dzanja lao.


Ndipo ngati mupatsa moni abale anu okhaokha, muchitanji choposa ena? Kodi angakhale anthu akunja sachita chomwecho?


ndipo pakukhala nanu, ndi kusowa, sindinasaukitse munthu aliyense; pakuti abale akuchokera ku Masedoniya, anakwaniritsa kusowa kwanga; ndipo m'zonse ndinachenjera ndekha, ndisalemetse inu, ndipo ndidzachenjerapo.


Pakuti kuli chiyani chimene munachepetsedwa nacho ndi Mipingo yotsala ina, ngati si ichi kuti ine ndekha sindinasaukitse inu? Ndikhululukireni choipa ichi.


Ndipo idzatenga limodzi la magawo khumi la mbeu zanu, ndi la minda yanu yampesa, nidzalipatsa akapitao ake, ndi anyamata ake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa