Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;
Masalimo 74:1 - Buku Lopatulika Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Inu Mulungu, chifukwa chiyani mukutitaya mpaka muyaya? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutirira nkhosa za busa lanu ngati moto? Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chiyani mwatitaya ife kwamuyaya, Inu Mulungu? Chifukwa chiyani mkwiyo wanu ukutukutira pa nkhosa za busa lanu? |
Ndipo ndidzataya chotsala cha cholowa changa, ndi kuwapereka m'dzanja la adani ao, nadzakhala iwo chakudya ndi chofunkha cha adani ao onse;
Dziwani kuti Yehova ndiye Mulungu; Iyeyu anatilenga, ndipo ife ndife ake; ndife anthu ake ndi nkhosa zapabusa pake.
Unakwera utsi wotuluka m'mphuno mwake, ndi moto wa m'kamwa mwake unanyeka nuyakitsa makala.
Udziweramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m'kati mwanga? Yembekeza Mulungu; pakuti ndidzamlemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.
Ndidzati kwa Mulungu, thanthwe langa, mwandiiwala chifukwa ninji? Ndimayenderanji wakulira chifukwa cha kundipsinja mdaniyo?
Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.
Chifundo chake chalekeka konsekonse kodi? Lonjezano lake lidatha kodi ku mibadwo yonse?
Potero ife anthu anu ndi nkhosa zapabusa panu tidzakuyamikani kosatha; tidzafotokozera chilemekezo chanu ku mibadwomibadwo.
Pakuti Iye ndiye Mulungu wathu, ndipo ife ndife anthu a pabusa pake, ndi nkhosa za m'dzanja mwake. Lero, mukamva mau ake!
Ndipo Mose anapemba kwa Yehova Mulungu wake, nati, Yehova, mtima wanu upserenji pa anthu anu, amene munawatulutsa m'dziko la Ejipito ndi mphamvu yaikulu, ndi dzanja lolimba?
Koma tsopano, Yehova, Inu ndinu Atate wathu; ife tili dongo, ndipo Inu ndinu Muumbi wathu; ndipo ife tonse tili ntchito ya dzanja lanu.
Atero Yehova, Ngati ukhoza kuyesa thambo la kumwamba, ndi kusanthula pansi maziko a dziko, pamenepo ndidzachotsa mbeu zonse za Israele chifukwa cha zonse anazichita, ati Yehova.
Ndipo inu nkhosa zanga, nkhosa zapabusa panga, ndinu anthu, ndi Ine ndine Mulungu wanu, ati Ambuye Yehova.
Pali Ine, ati Ambuye Yehova, zedi, popeza nkhosa zanga zinakhala nyama, ndi nkhosa zanga zinakhala chakudya cha zilombo zonse zakuthengo, chifukwa kunalibe mbusa, ndi abusa anga sanafunefune nkhosa zanga, koma abusawo anadzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga;
Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yake zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lake pansi pa thambo.