Masalimo 85 - Buku LopatulikaAkumbutsa Mulungu madalitso akale, apempha awabwereze Kwa Mkulu wa Nyimbo: Salimo la ana a Kora. 1 Munachita zovomereza dziko lanu, Yehova; munabweza ukapolo wa Yakobo. 2 Munachotsa mphulupulu ya anthu anu, munafotsera zolakwa zao zonse. 3 Munabweza kuzaza kwanu konse; munabwerera kumkwiyo wanu wotentha. 4 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife. 5 Kodi mudzatikwiyira nthawi zonse? Kodi mudzakhala chikwiyire mibadwomibadwo? 6 Kodi simudzatipatsanso moyo, kuti anthu anu akondwerere ndi Inu? 7 Tionetseni chifundo chanu, Yehova, tipatseni chipulumutso chanu. 8 Ndidzamva cholankhula Mulungu Yehova; pakuti adzalankhula zamtendere ndi anthu ake, ndi okondedwa ake; koma asabwererenso kuchita zopusa. 9 Indedi chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo akumuopa Iye; kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu. 10 Chifundo ndi choonadi zakomanizana; chilungamo ndi mtendere zapsompsonana. 11 Choonadi chiphukira m'dziko; ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba. 12 Inde Yehova adzapereka zokoma; ndipo dziko lathu lidzapereka zipatso zake. 13 Chilungamo chidzamtsogolera; ndipo chidzamkonzera mapazi ake njira. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi