Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 85:4 - Buku Lopatulika

4 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mutibweze, Mulungu wa chipulumutso chathu, nimuletse udani wanu wa pa ife.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Mutibwezerenso mwakale, Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Tibwezeretseninso mwakale Inu Mulungu Mpulumutsi wathu, ndipo mutichotsere mkwiyo wanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 85:4
17 Mawu Ofanana  

Mulungu wanga, ndakhulupirira Inu, ndisachite manyazi; adani anga asandiseke ine.


Yehova ndiye kuunika kwanga ndi chipulumutso changa; ndidzaopa yani? Yehova ndiye mphamvu ya moyo wanga; ndidzachita mantha ndi yani?


Koma Iye pokhala ngwa chifundo, anakhululukira choipa, osawaononga; nabweza mkwiyo wake kawirikawiri, sanautse ukali wake wonse.


Mutibweze, Yehova Mulungu wa makamu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


Mutibweze, Mulungu; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


Mulungu wa makamu, mutibweze; nimuwalitse nkhope yanu, ndipo tidzapulumuka.


Pakuti patsala kamphindi, ndipo ukali udzathedwa ndi mkwiyo wanga wakuwaononga.


Tsiku lomwelo udzati, Ndikuyamikani inu Yehova; pakuti ngakhale munandikwiyira, mkwiyo wanu wachoka, ndipo mutonthoza mtima wanga.


Kumva ndamva Efuremu alinkulirira kotero, Mwandilanga ine, ndipo ndalangidwa, monga mwanawang'ombe wosazolowera goli; munditembenuze ine, ndipo ine ndidzatembenuka; pakuti inu ndinu Yehova Mulungu wanga.


Mutitembenuzire kwa Inu, Yehova, ndipo tidzatembenuzidwadi, mukonzenso masiku athu ngati kale lija.


Ambuye, monga mwa chilungamo chanu chonse, mkwiyo wanu ndi ukali wanu zitembenuketu, zichoke kumzinda wanu Yerusalemu, phiri lanu lopatulika; pakuti mwa zochimwa zathu, ndi mphulupulu za makolo athu, Yerusalemu ndi anthu anu asanduka chotonza cha onse otizungulira.


Sindidzachita mkwiyo wanga waukali, sindidzabwerera kuononga Efuremu; pakuti Ine ndine Mulungu, si munthu ai; Woyera wa pakati pako; ndipo sindidzalowa m'mzinda.


Koma ine, ndidzadikira Yehova; ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.


Ndipo adzabwezera mitima ya atate kwa ana, ndi mitima ya ana kwa atate ao; kuti ndisafike ndi kukantha dziko lionongeke konse.


Inu mulambira chimene simuchidziwa; ife tilambira chimene tichidziwa; pakuti chipulumutso chichokera kwa Ayuda.


Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa