Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 85:9 - Buku Lopatulika

9 Indedi chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo akumuopa Iye; kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Indedi chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo akumuopa Iye; kuti m'dziko mwathu mukhale ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Zoonadi, Mulungu ali wokonzekera kuti apulumutse amene amamuwopa, kuti ulemerero wake ukhale m'dziko lathu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Ndithu chipulumutso chake chili pafupi ndi iwo amene amaopa Iye, kuti ulemerero wake ukhale mʼdziko lathu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 85:9
22 Mawu Ofanana  

Chipulumutso chitalikira oipa; popeza safuna malemba anu.


Wopereka nsembe yachiyamiko andilemekeza Ine; ndipo kwa iye wosunga mayendedwe ake ndidzamuonetsa chipulumutso cha Mulungu.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


ndiyandikizitsa chifupi chilungamo changa sichidzakhala patali, ndipo chipulumutso changa sichidzachedwa; ndipo ndidzaika chipulumutso m'Ziyoni, cha kwa Israele ulemerero wanga.


Mudzatero yense kwa mnansi wake, ndi yense kwa mbale wake, Yehova wayankha chiyani? Ndipo Yehova wanena chiyani?


Uzitero kwa mneneri, Yehova wakuyankha chiyani? Ndipo Yehova wanenanji?


Pakuti ndidziwa malingiriro amene ndilingiririra inu, ati Yehova, malingiriro a mtendere, si a choipa, akukupatsani inu adzukulu ndi chiyembekezero.


pamenepo ndidzakutsitsa nao otsikira kumanda, kwa anthu a kale lomwe, ndi kukukhalitsa kumalo a kunsi kwa dziko, kopasukira kale lomwe, pamodzi nao otsikira kumanda, kuti mwa iwe musakhale anthu; ndipo ndidzaika ulemerero m'dziko la amoyo,


Ananenanso nane, Wobadwa ndi munthu iwe, mau anga onse ndidzawanena ndi iwe uwalandire m'mtima mwako, utawamva m'makutu mwako.


Ndidzaima pa dindiro langa ndi kudziika palinga, ndipo ndidzayang'anira ndione ngati adzanenanji mwa ine, ngatinso ndidzamyankha chiyani pa choneneza changa.


Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.


Pakuti atero Yehova wa makamu: Utatha ulemererowo ananditumiza kwa amitundu amene anakufunkhani; pakuti iye wokhudza inu, akhudza mwana wa m'diso lake.


kuunika kukhale chivumbulutso cha kwa anthu a mitundu, ndi ulemerero wa anthu anu Israele.


Ndipo Mau anasandulika thupi, nakhazikika pakati pa ife, ndipo tinaona ulemerero wake, ulemerero wonga wa wobadwa yekha wa Atate, wodzala ndi chisomo ndi choonadi.


Ngati munthu aliyense afuna kuchita chifuniro chake, adzazindikira za chiphunzitsocho, ngati chichokera kwa Mulungu, kapena ndilankhula zochokera kwa Ine ndekha.


Ndipo Paulo ananyamuka, nakodola ndi dzanja, nati, Amuna a Israele, ndi inu akuopa Mulungu, mverani.


Chifukwa chake Eli anati kwa Samuele, Pita, ukagone; ndipo akakuitananso, ukavomere, kuti, Nenani, Yehova, popeza mnyamata wanu akumva. Chomwecho Samuele anakagona m'malo mwake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa