Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 85:11 - Buku Lopatulika

11 Choonadi chiphukira m'dziko; ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Choonadi chiphukira m'dziko; ndi chilungamo chasuzumira chili m'mwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Anthu ake adzakhala okhulupirika pansi pano, ndipo Mulungu wakumwamba adzaŵalungamitsa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Kukhulupirika kumatumphuka kuchokera ku dziko lapansi, ndipo chilungamo chimayangʼana pansi kuchokera kumwamba.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 85:11
12 Mawu Ofanana  

Mapiri adzatengera anthu mtendere, timapiri tomwe, m'chilungamo.


Tsiku limenelo mphukira ya Yehova idzakhala yokongola ndi ya ulemerero, chipatso cha nthaka chidzakhala chokometsetsa ndi chokongola, kwa iwo amene adzapulumuka a Israele.


Chinakondweretsa Yehova chifukwa cha chilungamo chake kukuza chilamulo, ndi kuchilemekeza.


Igwani pansi, inu m'mwamba, kuchokera kumwamba, thambo litsanulire pansi chilungamo; dziko lapansi litseguke, kuti libalitse chipulumutso, nilimeretse chilungamo chimere pamodzi; Ine Yehova ndinachilenga chimenecho.


Pakuti ameneyo adzaphuka pamaso pake ngati mtengo wanthete, ndi ngati muzu womera m'nthaka youma; Iye alibe maonekedwe, pena kukongola; ndipo pamene timuona palibe kukongola kuti timkhumbe.


Akali chilankhulire, onani, mtambo wowala unawaphimba iwo: ndipo onani, mau ali kunena mumtambo, Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera, mverani Iye.


ndipo onani, mau akuchokera kumiyamba akuti, Uyu ndiye mwana wanga wokondedwa, mwa Iyeyu ndikondwera.


Ulemerero ukhale kwa Mulungu Kumwambamwamba, ndi mtendere pansi pano mwa anthu amene akondwera nao.


Yesu ananena naye, Ine ndine njira, ndi choonadi, ndi moyo. Palibe munthu adza kwa Atate, koma mwa Ine.


Ameneyo sanadziwe uchimo anamyesera uchimo m'malo mwathu; kuti ife tikhale chilungamo cha Mulungu mwa Iye.


kuti uyamikidwe ulemerero wa chisomo chake, chimene anatichitira ife kwaufulu mwa Wokondedwayo.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa