Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 78:1 - Buku Lopatulika

1 Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Tamverani, anthu anga, chilamulo changa; tcherezani khutu lanu mau a pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mvetsetsani zimene ndikukuphunzitsani, inu anthu anga. Tcherani khutu, mumve mau a pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Inu anthu anga imvani chiphunzitso changa; mvetserani mawu a pakamwa panga.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 78:1
12 Mawu Ofanana  

Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Imvani, anthu anga, ndipo ndidzanena; Israele, ndipo ndidzachita mboni pa iwe, Ine Mulungu, ndine Mulungu wako.


Pa Inu, Inu nokha, ndinachimwa, ndipo ndinachichita choipacho pamaso panu; kuti mukhale wolungama pakulankhula Inu, mukhalenso woyera pa kuweruza kwanu.


Mulungu, munatitayiranji chitayire? Mkwiyo wanu ufukiranji pa nkhosa za kubusa kwanu?


Tchera makutu ako, numvere mau a anzeru, nulozetse mtima wako kukadziwa zanga.


Mverani Ine, inu anthu anga, ndi kunditcherera makutu, iwe, mtundu wa anthu anga; pakuti lamulo lidzachokera kwa Ine, ndipo ndidzakhazikitsa chiweruziro changa chikhale kuunika kwa anthu.


Tcherani khutu lanu, mudze kwa Ine, imvani, mzimu wanu nudzakhala ndi moyo; ndipo ndidzapangana nanu chipangano chosatha, ndicho zifundo zoona za Davide.


Amene ali ndi makutu, amve.


Imvani mafumu inu; tcherani makutu, akalonga inu; ndidzamuimbira ine Yehova, inetu; ndidzamuimbira nyimbo, Yehova, Mulungu wa Israele.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa